Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JULY 16, 2015
GERMANY

Bambo Wina ndi Mwana Wake Analandira Mendulo Yaulemu Chifukwa Chopulumutsa Anthu pa Ngozi ya Galimoto

Bambo Wina ndi Mwana Wake Analandira Mendulo Yaulemu Chifukwa Chopulumutsa Anthu pa Ngozi ya Galimoto

Jorim, mayi ake ndi a Bonk. Pa nthawi ya mwambowu a Bonk anali kuchipatala pa chifukwa china chosagwirizana ndi nkhaniyi.

SELTERS, Germany—A Andreas Bonk, omwe ndi a Mboni za Yehova, ndi mwana wawo Jorim anali m’gulu la anthu amene analandira mamendulo aulemu pa 16 April 2015. Anthuwa analandira mamendulowo chifukwa chothandiza kupulumutsa anthu atatu omwe anali m’galimoto yomwe inachita ngozi n’kuyamba kuyaka. Pamwambowo panali nduna ya za m’dziko ya chigawo cha Baden-Württemberg, ku Germany, ndiponso meya wa mzinda wa Obersulm ndi wa Waiblingen, kwawo kwa olandira mamendulowo. Nduna ya za M’dziko a Reinhold Gall (chithunzi cham’mwamba, wachitatu kuchokera kumanja) anapereka kwa a Andreas Bonk mendulo chifukwa chopulumutsa anthu a m’chigawo chawo. Mkazi wa a Bonk (chithunzi cham’mwamba, ali pakatiyo) analandira menduloyo m’malo mwa mwamuna wake chifukwa chakuti anali kuchipatala pa nthawi ya mwambowu. Anali kuchipatala pa chifukwa china chosagwirizana ndi nkhaniyi. Meya wa mzinda wa Obersulm, a Tilman Schmidt (chithunzi cham’mwamba, kumanzere), anapereka satifiketi yaulemu kwa Jorim Bonk (chithunzi cham’mwamba, pakati).

Pa 11 May 2014, a Bonk ndi mwana wawo Jorim anali pa ulendo wopita kumsonkhano waukulu wa Mboni za Yehova komwe a Bonk ankafunika kukakamba nkhani yochokera m’Baibulo. Panjira anapeza galimoto itachita ngozi n’kuyamba kuyaka. Asilikali 4 a ku United States anali m’galimotoyo ndipo ankakanika kutuluka. A Bonk ndi mwana wawoyo komanso anthu ena awiri, anaima kuti athandize anthuwo. A Andreas Bonk anaika moyo wawo pa ngozi kuti athandize anthuwo kutuluka m’galimotoyo mpaka pamene apolisi, ozimitsa moto ndiponso achipatala anafika. Koma n’zomvetsa chisoni kuti msilikali mmodzi anamwalira. Nyuzipepala ina inafotokoza kuti a Gall anauza anthu opulumutsa anzawowo kuti, “Munachita zinthu molimba mtima, mopanda mantha ndiponso mosaganizira za moyo wanu.” A Schmidt anawonjezera kuti, “Anthu tonse a ku Obersulm, timakunyadirani kwambiri.”

Chithunzi cha ngoziyo.

A Bonk anafotokoza chimene chinawachititsa kuti alimbe mtima kuthandiza anthuwo. Anati: “Ndinaima kuti ndiwathandize chifukwa chowadera nkhawa. Ndimaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wamtengo wapatali. . . . Ngati ineyo kapena m’bale wanga atachita ngozi, ndingakonde kuti anthu ena alimbe mtima n’kuwathandiza.” Jorim anawonjezera kuti, “Sitikuyenera kumanyalanyaza anthu amene akufunikira thandizo.”

Mwambowu unachitikira muholo yaikulu yamumzinda wa Obersulm. Nyuzipepala ina ya ku Germany inafotokoza mmene mwambowu unayendera ndipo inafotokoza mawu amene meya wa mzinda wa Waiblingen, dzina lake Andreas Hesky (chithunzi cham’mwamba, wachiwiri kuchokera kumanja), ananena. Anati: “Mukakumbukira zimene munachitazo muzinyadira kwambiri. Anthu a ku Waiblingen ndi osangalala kwambiri kukhala ndi anthu ngati inu. Ndinu chitsanzo chabwino kwambiri.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 500

Germany: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110