Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

APRIL 29, 2016
ECUADOR

Chivomezi Chimene Chinachitika M’dziko la Ecuador

Chivomezi Chimene Chinachitika M’dziko la Ecuador

Pa 16 April, 2016, m’dera lina la m’mphepete mwa nyanja ya Pacific m’dziko la Ecuador, munachitika chivomezi champhamvu kwambiri ndipo chinali cha phokoso. Chivomezicho komanso zivomezi zina zing’onozing’ono zimene zinachitika pambuyo pake, zinapha anthu oposa 650 ndi kuononga zinthu zambiri. Ngakhale kuti ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dzikoli sinawonongeke, nyumba zambiri za a Mboni m’derali zinawonongeka. Malipoti aposachedwapa atsimikiza kuti wa Mboni mmodzi[wamkazi] anafa. A Mboni atumiza magalimoto oti akapereke chakudya komanso madzi akumwa m’dera limene lakhudzidwa ndi ngoziyi. Ofesi ya nthambi inatumiza makomiti awiri kuti ayang’anire ndi kuyendetsa ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndipo anakhazikitsa malo awiri othandizirako anthuwo. Malo ena ali mu mzinda wa Pedernales ndipo ena ali mu mzinda wa Manta. Kuwonjezera pamenepo, anthu 4 ochokera ku ofesi ya nthambi anapita ku deralo kukaona anthu omwe anakhudzidwa komanso kukawalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Ecuador: Marco Brito, tel. +593 98 488 8580