NEW YORK—Pa August 1, 2014, a Mboni za Yehova padziko lonse anayamba kugawira kapepala katsopano kakuti Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo? Cholinga cha kapepalaka ndi kudziwitsa anthu za webusaiti yawo yovomerezeka ya jw.org. Webusaitiyi yamasuliridwa m’zinenero pafupifupi 500 komanso pali mabuku ndi zinthu zomwe zikhoza kupangidwa dawunilodi m’zinenero pafupifupi 700. Padziko lonse palibenso webusaiti imene yamasuliridwa m’zinenero zambiri kuposa ya jw.org.

Tsiku lililonse anthu oposa 1 miliyoni amatsegula wabusaiti ya jw.org. Pawebusaitiyi pali nkhani komanso mavidiyo amene amapereka malangizo othandiza kwa anthu a misinkhu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Vidiyo ina, yamutu wakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?, yapangidwa linki ku kachidindo ka QR komwe kali pakapepala kodziwitsa anthu za webusaitiyi moti munthu akhoza kuitsegula akangopanga sikani kachidindoka. M’vidiyoyi muli zithunzi zenizeni komanso zongoyerekezera zosonyeza ubwino wophunzira Baibulo. Pakali pano vidiyoyi ikupezeka m’zinenero zoposa 450 ndipo yapangidwapo dawunilodi maulendo pafupifupi 4 miliyoni kuchokera nthawi imene inatulutsidwa pa 18 November 2013.

Bambo J. R. Brown, omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku malikulu awo omwe ali ku Brooklyn, mumzinda wa New York, ananena kuti: “Tikusangalala kwambiri ndi ntchito imeneyi. Padziko lonse pali a Mboni za Yehova pafupifupi 8 miliyoni ndipo mwezi uno tonse tiziuza anthu za webusaiti imeneyi. Kapepala kodziwitsa anthu za webusaitiyi kakhoza kugawiridwa kwambiri kuposa timapepala tonse timene takhala tikugawira.”

Bambo Geoffrey Jackson, omwe ndi membala wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anati: “Kuyambira nthawi imene webusaitiyi inakhazikitsidwa, zomwe ndi zaka ziwiri zapitazo, anthu padziko lonse aona kuti webusaiti yathu ya jw.org ndi yothandiza kwambiri. Pawebusaitiyi pali mavidiyo omwe angathandize ana anu, pali nkhani zimene zingathandize banja lanu komanso mukhoza kuwerenga Baibulo lomwe lili pa webusaitiyi. Tikufuna kuti anthu ambiri apindule ndi webusaiti ya jw.org. N’chifukwa chake mwezi uno tikugwira ntchito yodziwitsa anthu za webusaitiyi.”

Kuchokera m’mayiko ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000