Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 9, 2014
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Zimene a Mboni za Yehova Akuchita Polimbana ndi Ebola

Zimene a Mboni za Yehova Akuchita Polimbana ndi Ebola

NEW YORK—Pamene matenda a Ebola akupitirizabe kufalikira komanso kupha anthu ambiri Kumadzulo kwa Africa, a Mboni za Yehova akuyesetsa kuphunzitsa anthu m’mipingo yawo za mmene angapewere matendawa.

Atangodziwa kuti matenda a Ebola ayamba ku Guinea ndipo akufalikiranso m’mayiko oyandikana nawo a Liberia ndi Sierra Leone, maofesi a Mboni za Yehova m’mayikowa analembera mipingo yonse makalata owadziwitsa za matendawa. Mogwirizana ndi malangizo a azaumoyo m’mayikowa, makalatawo anafotokoza kuopsa kwa matendawa, mmene anthu angawatengere, mmene angawapewere komanso zimene angachite kuti asawafalitse. Collin Attick yemwe amalankhula moimira a Mboni za Yehova ku Sierra Leone, ananena kuti: “Poyamba anthu sankadziwa zomwe angachite chifukwa chosokonezeka maganizo ndi nkhani zabodza zokhudza zimene zimayambitsa matenda a Ebola komanso chifukwa choti anthu ambiri sakonda kupita kuchipatala. Koma a Mboni atamva malangizo ku Nyumba ya Ufumu, anayamba kuwagwiritsira ntchito nthawi yomweyo.”

Mu July, anthu amene anatumidwa ndi ofesi ya Mboni za Yehova anayamba kuyendera mipingo ya ku Sierra Leone ndi Guinea kuti akalimbikitse mipingoyo. Iwo ankakamba nkhani ya mutu wakuti “Kumvera Kumapulumutsa.” Cholinga cha nkhaniyi chinali kuthandiza anthu kuti adziwe njira zomwe zingawathandize kupewa matendawa komanso kuwalimbikitsa kuti apitirize kutsatira malangizo alionse amene angapatsidwe. Oimira ofesi ya Mboniwa apitiriza kuyendera mipingoyi mpaka mu November 2014. A Mboni za Yehova ku Guinea, Liberia, ndi Sierra Leone, anakonza malo osambira m’manja paliponse pamene pali nyumba zawo zolambirira (kapena kuti Nyumba za Ufumu). Ndipo madzi osamba m’manja anawasakaniza ndi mankhwala opha majeremusi. A Mboni za Yehova ambiri m’mayikowa ayamba kuchitanso zofananazi m’nyumba zawo.

Pofuna kuthandiza kuti matenda a Ebola asafalikire, banja la Mboni za Yehova linalolera kukakhala ku tawuni ya Dolo komwe kuli malo osungira anthu omwe akuwaganizira kuti angakhale ndi matendawa. Malowa anakhazikitsidwa pa September 8, 2014, kummawa kwa Monrovia, m’dziko la Liberia.

Lipoti la Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse la pa October 1, 2014, linasonyeza kuti pa anthu 7,178 omwe anagwidwa ndi matendawa, anthu opitirira 3,300 anamwalira. Ndipo pali chiyembekezo chakuti ziwerengerozi ziwonjezereka. Lipoti la pa October 2 linasonyeza kuti m’mayiko a Guinea ndi Sierra Leone muli Mboni za Yehova zokwana 2,800 ndipo wa Mboni mmodzi yemwenso amagwira ntchito ya unesi anadwala matendawa ndipo anamwalira pa September 25, 2014. Ku Liberia, kuli a Mboni okwana 6,365 ndipo 10 anamwalira ndi matendawa. Pa anthu omwe anamwalirawa, 6 anali ogwira ntchito zachipatala. Matendawa anafikanso ku Nigeria, koma palibe wa Mboni amene anapezeka nawo. Pamene matendawa amayamba m’mayikowa, n’kuti amishonale ambiri atapita ku Europe ndi ku United States kukachita misonkhano kapenanso kutchuthi, choncho palibe mmishonale amene anadwala. Posachedwapa, a Mboni ena amene akuchita umishonale m’mayikowa anabwera kutchuti komanso kumsonkhano ndipo akuyesetsa kutsatira malangizo amene ofesi ya Mboni ya m’dziko limene akukhala ikupereka. Amishonale ena akudikirabe pa zifukwa zina kapenanso chifukwa chakuti m’mayiko ena maulendo a pandege anaimitsidwa kaye.

Malo osambira m’manja pa Nyumba ya Ufumu ya ku Sierra Leone.

Makomiti a Mboni othandiza pakachitika ngozi akuthandiza a Mboni anzawo a m’mayiko omwe akhudzidwa kwambiri ndi Ebola. A Thomas Nyain,  Sr, omwe amalankhula moimira Mboni wa Yehova ku Liberia anati: “Kutsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza ukhondo ndi kupatula anthu omwe ali ndi matenda opatsirana kwathandiza kwambiri kuti matendawa asafalikire. Timapewanso miyambo yoikira maliro yosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zikuthandiza kwambiri a Mboni za Yehova tonse, makamaka pa nthawi yovutayi.”

Pa siteshoni ya wailesi ina ku Sierra Leone, analengeza zomwe a Mboni za Yehova achita pothandiza a Mboni ndi anthu ena onse amene akukhala m’dera limene muli Ebola. Akuluakulu a boma anapemphanso kuti makomiti a Mboni othandiza pakachitika ngozi, agwire ntchito limodzi ndi anthu otumidwa ndi boma.

Bambo J. R. Brown, omwe amalankhula moimira Mboni za Yehova ku likulu lawo ku New York, ananena kuti: “Timalimbikitsidwa kwambiri tikamamva mmene a Mboni anzathu akuyesetsera kumvera malangizo ndi kupitiriza kulambira komanso kuphunzitsa anthu Baibulo. Nthawi zonse timaganizira komanso kupempherera abale athu amene akuvutika chifukwa cha matenda a Ebola.”

Kuchokera Kumayiko Ena:

Lankhulani ndi: J.R.Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Guinea: Thierry Pourthié, tel. +224 631 40 96 50

Liberia: Thomas Nyain, Sr., tel. +231 886 513 414

Nigeria: Paul Andrew, tel. +234 7080 662 020

Sierra Leone: Collin Attick, tel. +232 77 850 79