NEW YORK—Msonkhano woyambirira pa misonkhano yamayiko, yomwe a Mboni za Yehova amachita kwa masiku atatu, unayamba Lachisanu m’mawa pa June 6, 2014, ku Ford Field m’dera la Detroit, m’chigawo cha Michigan ku USA. Mutu wa msonkhanowu ndi wakuti, “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba.” Nkhani zina pa msonkhanowu zizionetsedwa pa vidiyo ya pa Intaneti kumadera ena monga ku Arizona, California, Florida, Illinois, Missouri, New Jersey ndiponso North Carolina. Komanso nkhanizi zizimasuliridwa m’zinenero za Chiabaniya, Chikoreya, Chipolishi ndi Chipwitikizi.

Bambo J. R. Brown, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova kulikulu lawo lapadziko lonse ku Brooklyn, New York, anati: “Kwa milungu itatu yapitayi, a Mboni ku Detroit komanso a m’madera ena omwe adzamvetsere msonkhanowu pa vidiyo ya pa Intaneti, akhala akugwira ntchito yoitanira anthu kumsonkhano wapaderawu. Kumsonkhano womwe udzachitikire ku Detroit, tikuyembekezera kuti kudzafika anthu osachepera 45,000, azikhalidwe zosiyanasiyana. Tikuyembekezeranso kuti kudzafika nthumwi zoposa 2,000 zochokera kumayiko ena, monga ku Australia, Canada, Germany ndi ku Taiwan.”

M’nyengo yonse yotetha, a Mboni za Yehova ku United States akhala akuchita misonkhano ya mayiko yokwana 16. Misonkhanoyi izichitikira m’masitediyamu akuluakulu omwe ali m’madera 10 m’dzikolo. M’madera ena, nkhani zonse za pamsonkhanowu, kapena nkhani zochepa chabe, zizidzakambidwa m’zinenero zosiyanasiyana monga, Chiabaniya, Chinenero Chamanja cha ku America, Chiarabu, Chiameniya, Chikantonizi, Chichuki, Chifulenchi, Chigiriki, Chikiliyo cha ku Haiti, Chihindi, Chiiloko, Chiindoneziya, Chitaliyana, Chijapanizi, Chikoreya, Chimandarini, Chimasho, Chiperisiya, Chipolishi, Chiromaniya, Chirasha, Chisamowa, Chisipanishi, Chitagalogi, Chitwi ndi Chivetinamu. Kuyambira mu June 2014 mpaka mu 2015, a Mboni za Yehova akhala akuchita misonkhanoyi ku Australia, Ecuador, England, Germany, Greece, Mexico, South Korea, ndi Zimbabwe.

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000