Pamwambowu padzakambidwa nkhani yofotokoza mfundo za m’Baibulo.

NEW YORK—Loweluka pa 27 February, a Mboni za Yehova padziko lonse adzayamba kugwira ntchito yapadera yoitanira anthu ku mwambo umene amauona kuti ndi wofunika kwambiri pa chaka. Mwambowu ndi wokumbukira imfa ya Yesu ndipo udzachitika pa 23 March. Bambo David A. Semonian, omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova kulikulu lawo ku New York anati: “Pamwambowu padzakambidwa nkhani yofotokoza mmene imfa ya Yesu ilili yofunika masiku ano ngakhale kuti inachitika zaka 2000 zapitazo. Nkhaniyi idzafotokozanso mmene imfayi imatipatsira chiyembekezo cha mtsogolo. Tikufunitsitsa kuti anthu ambiri adzabwere n’cholinga choti adzapindule ndi malangizo a m’Baibulo omwe adzafotokozedwe pa mwambowu.”

A Mboni okwana 8 miliyoni padziko lonse adzagwira nawo ntchito yoitanira anthu ku mwambowu. Chaka chatha, anthu amene anapezeka pa mwambowu analipo pafupifupi 20 miliyoni

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000