Pitani ku nkhani yake

MARCH 6, 2018
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni Ayamba Kugwira Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu Kuti Adzakhale Nawo pa Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu

A Mboni Ayamba Kugwira Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu Kuti Adzakhale Nawo pa Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu

Pa 3 March, 2018, a Mboni za Yehova padziko lonse anayamba ntchito yapadera yogawira timapepala toitanira anthu ku mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, womwe umadziwikanso kuti Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Pa 31 March, a Mboni m’mayiko okwana 240 adzasonkhana kuti achite mwambowu womwe amauona kuti ndi mwambo wofunika kwambiri pachaka. A Mboni akuitaniranso anthu kuti adzamvetsere nawo nkhani yapadera ya m’Baibulo ya mutu wakuti “Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani Kwenikweni?” Nkhani yapaderayi idzakambidwa mlungu woyambira 19 March.

A David A. Semonian, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova anati: “Mu 2017, anthu oposa 20 miliyoni anachita nawo mwambo wa Chikumbutso, ndipo anthu 12 miliyoni sanali a Mboni. Choncho mwambo wa Chikumbutso womwe umachitika chaka chilichonse, sikuti ndi wofunika kwa Mboni za Yehova zokha koma ndi wofunikanso kwa anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse. Cholinga chathu n’choti anthu onse alandire kapepalaka kuti adzachite nawo mwambowu pamalo akufupi ndi komwe ali.”

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000