Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Webusaiti Yathu Yovomerezeka Yakonzedwanso

Webusaiti Yathu Yovomerezeka Yakonzedwanso

Kwa miyezi ingapo yapitayi, gulu la anthu 40 a Mboni za Yehova ku New York lakhala likugwira ntchito mothandizana ndi Dipatimenti Yojambula Zithunzi komanso Dipatimenti Yolemba Nkhani pokonzanso webusaiti ya www.jw.org. Cholinga chake n’chakuti webusaitiyi ikhale yokongola kwambiri ndiponso yosavuta kugwiritsa ntchito, kaya pakompyuta kapena pazipangizo zina zing’onozing’ono monga foni ya m’manja. Koma pali zifukwa zinanso ziwiri zimene zachititsa kuti webusaitiyi ikonzedwenso.

1. Taphatikiza mawebusaiti athu onse. Mawebusaiti atatu a Mboni za Yehova tawaphatikiza n’kupanga webusaiti imodzi ya www.jw.org. Zimenezi zikutanthauza kuti mawebusaiti awiri enawo, omwe ndi www.watchtower.org ndiponso www.jw-media.org, sakhalaponso. Kuphatikiza mawebusaitiwa kuthandiza anthu kuti azipeza nkhani zonse zokhudza Mboni za Yehova pamalo amodzi. Mwachitsanzo, mungapeze, kumvetsera kapenanso kusindikiza masamba a Baibulo ndiponso a mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zinenero zambirimbiri.

2. Tawonjezerapo zinthu zina. Pawebusaiti yatsopanoyi pali mayankho achidule ndi osapita m’mbali a mafunso a nkhani za m’Baibulo. Komanso pali nkhani zina zokhudza Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, pali nkhani zokhudza ntchito yathu yolalikira, maofesi a nthambi, Nyumba za Ufumu ndiponso misonkhano yathu ikuluikulu. M’chigawo chakuti “Nkhani” muli nkhani zokhudza Mboni za Yehova padziko lonse. Pawebusaitiyi palinso nkhani zina zokambirana zokhudza mabanja, achinyamata ndiponso ana.

Tsiku lililonse, anthu masauzande ambirimbiri amawerenga mabuku a Mboni pa Intaneti m’zinenero zosiyanasiyana zokwana 430. Anthu ena amakopera zinthu zosiyanasiyana zomvetsera, ma EPUB, ma PDF ndiponso mavidiyo a chinenero chamanja. Tsiku ndi tsiku, anthu amakopera zinthu zimenezi zochuluka kwambiri pafupifupi 500,000. Komanso, tsiku lililonse anthu pafupifupi 100 amapempha kuti munthu wa Mboni za Yehova aziphunzira nawo Baibulo.