Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MARCH 13, 2014
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Akupanga Baibulo Latsopano Lalikulu

A Mboni za Yehova Akupanga Baibulo Latsopano Lalikulu

NEW YORK—Pofuna kuthandiza anthu ambiri kuti akhale ndi Baibulo, a Mboni za Yehova akupanga Baibulo lalikulu. Baibulo lalikululi ndi la Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe linakonzedwanso. Baibulo lalikululi likusindikizidwa ku United States ndi ku Japan ndipo pali mapulani akuti Mabaibulo omwe adzatulutsidwe koyambirira adzakhale okwana 424,000.

A Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la zilembo za nthawi zonse pa msonkhano umene unachitika pa October 5 mpaka 6, 2013. Msonkhanowu unalumikizidwa patelefoni ndi pa Intaneti m’mayiko 31. Baibulo limeneli, lomwe linakonzedwanso mu 2013, ndi labwino kwambiri kuposa Baibulo limene a Mboni za Yehova anatulutsa mu 1984. Pa October 7, 2013, a Mboni anaika Baibulo latsopanoli papulogalamu ya pakompyuta ndiponso ya pazipangizo za m’manja yotchedwa Laibulale ya JW. Pofika pano, pulogalamuyi yapangidwa dawunilodi maulendo pafupifupi 1.4 miliyoni. Kuwonjezera pamenepa, Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso likupezeka pawebusaiti ya www.jw.org m’mitundu yosiyanasiyana, monga PDF ndi EPUB.

Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso, kaya losindikizidwa kapena limene mungaone pa Laibulale ya JW ngakhalenso pa Intaneti, lili ndi malifalensi pafupifupi 60,000 padanga lapakati. Malifalensiwa ndi othandiza kwambiri kuti munthu amvetse bwino nkhani zimene akuwerenga m’Baibulo. Komanso m’Baibuloli muli zithunzi za kala, mapu osonyeza malo otchulidwa m’Baibulo, ndiponso matchati osonyeza mmene zinthu zina zinalili kalelo. Mulinso nkhani zakumapeto zofotokoza zinthu zosiyanasiyana, monga mfundo zimene anthu omasulira Baibulo amatsatira pogwira ntchitoyi. M’nkhani zakumapeto zimenezi mulinso mbiri yofotokoza zimene zinkachitika polemba Baibulo komanso politeteza kuti lifike m’nthawi ino.

Mu Baibulo la Dziko Latsopano lomwe linatulutsidwa mu 1984, munali dzina la Mulungu nthawi zokwana 7,000. Koma atafufuza m’mipukutu yakale kwambiri ya Baibulo, apeza kuti pali malo ena angapo pamene pakupezeka dzina la Mulungu, ndipo izi zasonyezedwa m’Baibulo latsopanoli, lomwe linakonzedwanso mu 2013. Mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwansoli muli malo atsopano okwana 6, omwe pakupezeka dzina la Mulungu. Dzinali labwezeretsedwa m’malo amenewa potsatira umboni womwe wapezeka m’mipukutu ya ku Nyanja Yakufa komanso m’mipukutu ina yakale kwambiri. Malo amene dzinali labwezeretsedwapo ndi awa: Oweruza 19:18; 1 Samueli 2:25; 6:3; 10:26; 23:14, 16. Nkhani ina yakumapeto ikufotokoza mmene dzina la Mulungu linkagwiritsidwira ntchito m’Chiheberi chakale komanso Chigiriki chakale. Nkhaniyo ikufotokozanso mmene dzinali likupezekera m’Mabaibulo ambirimbiri a masiku ano m’zinenero zochuluka zedi.

Kwa zaka zambiri, a Mboni akhala akusindikiza, kugawira, komanso kumasulira Baibulo la Dziko Latsopano. Ndipotu akatswiri ambiri amaphunziro amayamikira Baibuloli kuti linamasuliridwa molondola. Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi linatulutsidwa lathunthu koyamba mu 1961. Kenako mu 1963, nyuzipepala ya The New York Times inanena kuti Baibulo la Dziko Latsopano liyamba kupezekanso m’zinenero zina 6, potsatira zimene a Mboni alengeza pamsonkhano wawo umene unachitika kusitediyamu ya Yankee. Pofika pano, a Mboni amasulira Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenero zoposa 120. Koma m’zaka zaposachedwapa, Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inasankha zoti imasulirenso Baibulo la Dziko Latsopano n’cholinga choti ligwirizane ndi mmene chinenero chilili masiku ano. Komitiyi inasankhanso zoti ilembe momveka bwino mawu ena ovuta amene anali m’Baibulo. Izi zathandiza kuti Baibulo la Dziko Latsopano, limene lakonzedwansoli, likhale losavuta kuwerenga komanso losavuta kumvetsa.

Poikira ndemanga pa nkhaniyi, Bambo J. R. Brown, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova kulikulu lawo la padziko lonse, anati: “Kwa zaka zoposa 50 zapitazo, takhala tikusangalala kwambiri kulandira Mabaibulo a Dziko Latsopano. Koma panopa chisangalalo chake n’chodzaza tsaya chifukwa tangolandira kumene Baibulo la Dziko Latsopano limene lakonzedwanso. Cholinga chathu n’chakuti munthu aliyense azitha kumvetsa Malemba Opatulika. N’chifukwa chake Baibuloli lamasuliridwa ndi mawu olondola, aulemu, komanso amene munthu aliyense angathe kumva mosavuta.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000