Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MAY 15, 2014
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Alengeza Kuti Akhala ndi Misonkhano Yamayiko

A Mboni za Yehova Alengeza Kuti Akhala ndi Misonkhano Yamayiko

NEW YORK—A Mboni za Yehova alengeza zoti akhala ndi misonkhano yamayiko m’mizinda yosiyanasiyana padziko lonse lapansi. Misonkhanoyi iyamba mu June 2014 mpaka mu January 2015, ndipo msonkhano uliwonse uzichitika kwa masiku atatu. Misonkhano yoyambirira ichitika ku United States ndipo kenako idzachitika ku Australia, Ecuador, England, Germany, Greece, Mexico, South Korea, ndi Zimbabwe. Misonkhano ya mayikoyi ikamachitika, misonkhano yachigawo imene a Mboni amachita chaka ndi chaka m’malo ang’onoang’ono, izichitikanso.

Msonkhano woyambirira pa misonkhano yamayikoyi udzachitika pa June 6, 2014, ku Ford Field m’dera la Detroit, Michigan, USA. Tikuyembekezera kuti pamsonkhanowu padzafika anthu pafupifupi 45,500, ndipo anthu 2,500 adzakhala nthumwi zochokera m’mayiko ena.

Pamisonkhano yamayikoyi padzakhala nthumwi zochokera m’mayiko ena, ndipo pamisonkhano ina padzakhalanso amishonale ochokera m’madera ena. Bambo J. R. Brown, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova kulikulu lawo lomwe lili ku Brooklyn, New York, ananena kuti: “Misonkhano yathu yamayiko ndi yapadera komanso yosangalatsa kwambiri. Tikuganiza kuti anthu omwe si a Mboni amene adzafike pamisonkhanoyi adzasangalala nafe limodzi chifukwa tonse timakhala ngati achibale komanso mabwenzi. Ndipo zikuoneka kuti misonkhano imene tikuyembekezerayi ikhala yapadera zedi.”

Mutu wa misonkhano yamayikoyi ndi wakuti “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba.” Bambo Brown anafotokoza kuti “mfundo yofunika kwambiri pamisonkhanoyi ikhala yokhudza nkhani yaikulu yotchulidwa m’Baibulo. Kuwonjezera pamenepa, nkhani za pamisonkhanoyi zikafotokoza kwambiri mfundo zokhudzana ndi zinthu ziwiri zimene a Mboni za Yehova amazikhulupirira kwambiri. Chinthu choyamba n’chakuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kumwamba mu 1914, ndipo chachiwiri n’chakuti Yesu Khristu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulunguwo. Chosangalatsa china n’chakuti misonkhanoyi ikamachitika, padzakhala patapita zaka 100 chiyambire Ufumu wa Mulungu ukulamulira.”

Panopa, a Mboni akukonzekera ntchito yapadera imene idzachitike padziko lonse yoitanira anthu kumisonkhano yachigawo imene idzachitike m’dera lawo lomwelo. Pamisonkhano imeneyi, mofanana ndi mmene zimakhalira ndi misonkhano yawo yonse, sipadzakhala kulipira polowa komanso sipadzakhala kuyendetsa mbale yazopereka.

Misonkhano imeneyi, yomwe mutu wake ndi wakuti “Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba,” idzachitika m’malo osiyanasiyana komanso pa masiku osiyanasiyananso. Kuti mudziwe malo ndi masiku enieni amene misonkhanoyi idzachitike, mungafufuze pawebusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova, ya jw.org. Atolankhani omwe akufuna kudziwa zambiri angafunse ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dera lawo kuti awauze munthu amene akuyendetsa zokhudza misonkhanoyi m’deralo, yemwe angathe kumufunsa zambiri pa nkhani ya kulemba ndi kuulutsa nkhani zokhudza misonkhanoyi.

Lankhulani ndi:

Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000