Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MARCH 20, 2014
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Padziko Lonse Ayamba Kugwira Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu Kumwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu

A Mboni za Yehova Padziko Lonse Ayamba Kugwira Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu Kumwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu

NEW YORK—Loweruka pa, March 22, 2014, a Mboni za Yehova padziko lonse, anayamba ntchito yapadera yoitanira anthu kumwambo womwe a Mboniwo amauona kuti ndi wofunika kwambiri pachaka. Mwambowu umatchedwa kuti Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Chaka chatha, anthu 19,241,252 anasonkhana pa mwambo wapaderawu. A Mboni za Yehova akukhulupirira kuti chaka chinonso anthu ambiri adzafika pa mwambo wa Chikumbutso umene udzachitike pa Lolemba April 14,dzuwa litalowa.

Bambo J. R. Brown, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova kumalikulu awo ku New York anati: “Mosakaikira tikukhulupirira kuti omwe adzabwere ku mwambo wa Chikumbutso chaka chino, adzasangalala kwambiri. Zimenezi zikutilimbikitsa kuti tiitanire anthu ambiri kumwambo wapaderawu.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera M’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000