Pitani ku nkhani yake

APRIL 30, 2015
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Alengeza za Misonkhano Yachigawo ya 2015

A Mboni za Yehova Alengeza za Misonkhano Yachigawo ya 2015

NEW YORK—A Mboni za Yehova ku United States adzayamba misonkhano yachigawo ya 2015 pa May 22. Mutu wa misonkhanoyi ndi wakuti “Tsanzirani Yesu” ndipo ipitiriza kuchitika padziko lonse mpaka January 2016. A Mboni za Yehova adzagwira ntchito yoitanira anthu ku msonkhanowu kwa milungu itatu. Anthu sadzafunika kulipira ndalama kuti achite nawo msonkhanowu.

Bambo J. R. Brown, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku likulu lawo lapadziko lonse lomwe lili ku Brooklyn, New York, ananena kuti: “Mutu wa msonkhano wachigawo wa chaka chino ukusonyeza kuti Yesu Khristu, ndi wodziwika padziko lonse ndiponso ndi chitsanzo chabwino kwa anthu a misinkhu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Tikukhulupirira kuti anthu onse amene adzapezekepo adzasangalala kuphunzira mbali zochititsa chidwi zokhudza moyo wa Yesu.” Msonkhano wa chaka chino udzakhala ndi mavidiyo ogwira mtima komanso osangalatsa kwambiri amene angadzatithandize kutsanzira Yesu pa moyo wathu.

Kuti mudziwe malo ndi masiku a misonkhano ya chigawo ya 2015 yakuti “Tsanzirani Yesu,” onani pa webusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova ya jw.org. Atolankhani amene akufuna kudzafalitsa zokhudza msonkhanowu, angapite ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lawo ndipo angakakumane ndi mneneri wa Mboni za Yehova wa m’dzikolo.

Lankhulani ndi:

Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000