Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MARCH 19, 2014
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Bambo Guy H. Pierce Omwe Anali M’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova Anamwalira Lachiwiri pa March 18, ali ndi Zaka 79

Bambo Guy H. Pierce Omwe Anali M’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova Anamwalira Lachiwiri pa March 18, ali ndi Zaka 79

Bambo Guy H. Pierce omwe anali a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anamwalira Lachiwiri pa March 18, ali ndi zaka 79. Iwo anamwalirira kulikulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York.

Bambo Pierce asiya mkazi wawo Penny, ana 6 ndiponso zidzukulu zambiri. A Mboni za Yehova padziko lonse sadzawaiwala, chifukwa bambowa ankaona kuti anthu onse a Mboni ndi a m’banja limodzi.

M’chikalata chofotokoza za imfa ya Bambo Pierce chimene anzawo a m’Bungwe Lolamulira analemba, munali mawu akuti: “Tipitiriza kulimbikitsidwa pa zaka zikubwerazi tikamakumbukira mmene Bambo Pierce ankachitira zinthu molimba mtima komanso mokhulupirika.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

 

Onani Zambiri