A Mboni za Yehova akupitiriza kuthandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena amene akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi ku Congo. Kusefukira kwa madziku kunachitika pa mlungu wa December 26 m’tawuni ya Boma yomwe ili pa mtunda wa pafupifupi makilomita 470 kumwera cha kum’mawa kwa Kinshasa.

Mabanja okwana 39 a Mboni anakhudzidwa ndi madzi osefukirawo, ndipo mmodzi anafa chifukwa cha ngoziyo. Kuonjezera pamenepo, nyumba 5 za a Mboni zinawonongekeratu, pomwe zina 5 zinawonongeka pang’ono.

Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Congo inatumiza chakudya ndi zovala kwa a Mboni omwe anakhudzidwa m’chigawo cha kumadzulo kwa dzikolo kuti ziwathandize. A Mboni ochokera m’matawuni a Matadi ndi Muanda, omwe ali pa mtunda wa makilomita 80 kuchokera m’tawuni ya Boma, anadzipereka pantchito yothandiza a Mboni anzawo.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likutsogolera ntchito yothandiza a Mboni omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi, ku Congo. Iwo akuchita zimenezi kuchokera ku likulu lawo la padziko lonse ku Warwick, New York, pogwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka pothandiza pantchito yolalikira ya padziko lonse.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Democratic Republic of the Congo: Robert Elongo, +243-81-555-1000