Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JANUARY 13, 2015
CROATIA

A Mboni Anachita Nawo Chionetsero cha Mabuku Pamwambo Wodziwika Kwambiri ku Croatia

A Mboni Anachita Nawo Chionetsero cha Mabuku Pamwambo Wodziwika Kwambiri ku Croatia

ZAGREB, Croatia—Pa 11 mpaka 16 November, 2014, a Mboni za Yehova anachita nawo chionetsero cha mabuku chomwe n’chosaiwalika m’dzikoli. Pa chionetserochi panabwera anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana ndipo panaonetsedwa mabuku ambiri okhudza maphunziro komanso nkhani zina zosiyanasiyana. Pa mwambowu panabwera anthu pafupifupi 130,000.

Pulezidenti wa dziko la Croatia, dzina lake Ivo Josipović, wafika pa malo a Mboni za Yehova ndipo akutenga mabuku.

Pulezidenti wadzikoli dzina lake Ivo Josipović, anapita pamalo amene a Mboni za Yehova anaikapo mabuku awo ndipo atapereka moni anatenga mabuku ofotokoza za sayansi ndiponso Baibulo. Mabukuwa anali, The Origin of Life—Five Questions Worth Asking, Was Life Created? ndi lakuti, Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?

Malo ena amene a Mboni anakonza, panali mabuku komanso pankaonetsedwa mavidiyo othandiza achinyamata ndi makolo.

Pamalo a Mboniwa panali malo ena omwe anthu ankakonda kupitapo. Pamalowa m’pamene anthu ankaonera mavidiyo a makatuni kuchokera pa webusaiti ya jw.org. Mavidiyowa anakonzedwa kuti aziphunzitsa ana mfundo za m’Baibulo. Anthu omwe anabwera pamalowa ankakonda kutenga buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa. Bukuli lili ndi mfundo zothandiza achinyamata ndiponso makolo.

Olankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Croatia, dzina lake Josip Liović, ananena kuti: “Tikusangalala kwambiri poona kuti anthu ankachita chidwi ndi mabuku athu pa chionetserochi. Anthu anatenga mabuku oposa 7,500 ndipo izi si zimene tinkayembekezera. Tikukhulupirira kuti chaka chamawa anthu adzasangalalanso ndi mabuku athu tikamadzachita nawo mwambowu.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Croatia: Josip Liović, tel. +385 91 5336 511