Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JULY 25, 2014
CROATIA

A Mboni Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Balkans

A Mboni Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Balkans

ZAGREB, Croatia—Pofuna kuthandiza anthu okhudzidwa ndi madzi osefukira ku mayiko a Bosnia-Herzegovina, Croatia, ndi Serbia, a Mboni za Yehova anakonza makomiti oti athandize anthu okhudzidwa ndi mavutowa. Makomitiwa anakonzedwa ndi anthu omwe amagwira ntchito ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Germany. Mvula yamphamvu yomwe inagwa ku Balkans kuyambira pa May 13 mpaka pa 15, 2014, inachititsa kuti madzi asefukire koopsa ndipo inachititsanso kuti nthaka ing’ambike malo 3,000.

Makomiti othandiza anthu okhudzidwa ndi ngoziyo nthawi yomweyo anayamba kuthandiza anthu osowa pokhala powapatsa zakudya, zovala komanso anawamangira nyumba zoti ayembekezeremo ndipo ankawathandizanso anthuwo pa nkhani ya mayendedwe. Ngakhale kuti palibe munthu wa Mboni za Yehova yemwe anafa pa ngoziyi kapena kuvulala, koma nyumba 14 za a Mboniwa zinawonongeka kwambiri moti zina mwa nyumbazi zinatheratu. Ndipo madzi osefukirawo anawononga nyumba yolambiriramo ya a Mboniwa. Panopa makomitiwo ali mkati mokonza nyumba zomwe zinawonongeka ndiponso kumanga nyumba za anthu omwe nyumba zawo zinawonongekeratu.

Bambo Josip Liović, omwe amalankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Croatia anati: “Mtima uli pansi tsopano poona kuti palibe m’bale wathu yemwe wavulala ndi ngozi yoopsayi, komabe tikumva chisoni chifukwa anthu ena achibale awo komanso mabwenzi awo amwalira. Ndipo tikuyesetsa kutonthoza anthu omwe akhudzidwa ndi tsokali m’mayiko onse a ku Balkans. Tikuthokoza abale athu a ku Germany omwe abwera kudzatithandiza kupereka thandizoli kwa abale athu amene akhudzidwa ndi tsokali m’masabata komanso m’miyezi ikubwerayi.”

Kuchokera Kumayiko Ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Croatia: Josip Liović, tel. +385 91 5336 511

Serbia: Daniel Domonji, tel. +381 11 405 99 00