Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MAY 2, 2014
CHILE

Moto Wolusa Wawononga Zinthu ku Valparaíso, Chile

Moto Wolusa Wawononga Zinthu ku Valparaíso, Chile

PUENTE ALTO, Chile—Pa April 13, 2014, moto wolusa womwe unafalikira kwambiri chifukwa cha mphepo yamphamvu yochokera kunyanja ya Pacific, unawononga zinthu kwambiri mumzinda wa Valparaíso ku Chile. Motowu unapha anthu osachepera 15 komanso kuvulaza anthu ena 500. Nyumba pafupifupi 2,900 zinawonongekeratu, ndipo anthu oposa 10,000 akusowa pokhala.

Akuluakulu a ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Chile anena kuti pagulu la anthu amene afa pa ngoziyi, pali bambo wachikulire wa Mboni. Kuwonjezera pamenepa, nyumba za anthu 89 a Mboni zawonongeka. Anthu ambiri a Mboni za Yehova amene nyumba zawo zawonongeka ndi motowu akusungidwa m’nyumba za a Mboni anzawo. Ngoziyi itangochitika, akuluakulu a ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Chile anakhazikitsa komiti yomwe ikuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngoziyi. Padakali pano, magulu a anthu ongodzipereka ayamba kale ntchito yochotsa zinthu zomwe zawonongeka ndi motowo. Pa nthawi yoyenerera, anthuwa adzayamba ntchito yokonza nyumba pafupifupi 28 zimene zawonongeka ndi moto, za anzawo a Mboni.

Bambo Jason D. Reed, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Chile, anati: “Tikudandaula kwambiri tikaganizira mavuto amene abale athu akukumana nawo chifukwa cha moto wolusawu. Tikulira chifukwa m’bale wathu yemwe tinkalambira naye Mulungu wafa pa ngoziyi. Tikupemphereranso anthu onse omwe achibale awo kapena anzawo amwalira pa ngoziyi. Tipitiriza kuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi powapatsa zinthu zofunikira pa moyo wawo zimene tingakwanitse. Komanso tipitiriza kuwalimbikitsa kuti athe kupirira pa nthawi yovutayi.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Chile: Jason D. Reed, tel. +56 2 2428 2600