A Mboni za Yehova akuthandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena amene akhudzidwa ndi moto wa m’nkhalango, womwe wawononga mahekitala oposa 500,000 pakati ndi kum’mwera kwa dziko la Chile. Akuluakulu a boma akuti motowu, womwe wakhala ukuyaka kwa masabata awiri, ndi moto woopsa kwambiri m’mbiri yonse ya dzikolo.

Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Chile yanena kuti palibe wa Mboni aliyense amene wavulala kapena kufa ndi motowu. A Mboni ena anathawa m’nyumba zawo ndipo a Mboni anzawo ndi amene anawapatsa malo okhala.

Komanso, nyumba 5 za a Mboni zinawonongeka ndi motowo. Ofesi ya nthambi inakhazikitsa komiti yopereka chithandizo n’cholinga choti ifufuze zinthu zimene anthu omwe akhudzidwa akufunika.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi limene limayendetsa ntchito yothandiza anthu amene akufunika thandizo kuchokera ku likulu la padziko lonse. Bungweli limagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo pofuna kuthandiza ntchito yolalikira ya padziko lonse.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Chile: Jason Reed, +56-2-2428-2600