Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

SEPTEMBER 22, 2015
CANADA

Akuluakulu a Boma Kumpoto kwa Dziko la Canada Anayamikira a Mboni za Yehova Chifukwa cha Ntchito Yawo Yophunzitsa Baibulo

Akuluakulu a Boma Kumpoto kwa Dziko la Canada Anayamikira a Mboni za Yehova Chifukwa cha Ntchito Yawo Yophunzitsa Baibulo

TORONTO—M’miyezi ya September ndi October 2014, ofesi ya Mboni za Yehova ku Canada inakonza zoti pagwiridwe ntchito yapadera yophunzitsa anthu Baibulo. A Mboni pafupifupi 150 anadzipereka kugwira nawo ntchitoyi. Panakonzedwa zoti a Mboniwo akalalikire m’madera 35 a m’dzikoli omwe ali kutali kwambiri.

Anthu oposa 32,000 amakhala m’madera 35 a anthu olankhula Chiinukituti omwe a Mboni za Yehova analalikirako ndipo maderawo ndi omwe ali ndi timadontho tachikasu pamapuwa. Ntchito yapaderayi inagwiridwa m’madera akuluakulu awiri ndiponso dera lina limodzi lomwe lasonyezedwa ndi mtundu wobiriwira.

A Mboniwo anagawidwa m’magulu ndipo ankalalikira m’matauni ndiponso m’midzi m’zigawo zakumpoto kwa dzikoli mpaka m’zigawo zakumadzulo. Analalikiranso m’dera la Quebec lomwe kukula kwake ndi makilomita 3,300 ndipo lili kum’mawa kwa dzikoli. Anthu omwe anagwira nawo ntchitoyi ankalipira okha ndalama zoyendera paulendowu ndipo ena anawononga ndalama zambiri kulipira ndege.

Tauni ya Paulatuk ndi imodzi mwa matauni amene a Mboni analalikirako. Kuli anthu pafupifupi 300 ndipo tauniyi ili m’mbali mwa nyanja ya Beaufort yomwe ili m’chigawo cha kumpoto cha madera a zigawo za kumpoto chakumadzulo.

Ntchito yapaderayi isanayambike, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linavomereza kuti vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? imasuliridwe m’chilankhulo cha Chiinukituti. Chilankhulochi chimalankhulidwa ndi anthu pafupifupi 35,000 ku Canada ndipo ndi chilankhulo chimene anthu ambiri amagwiritsa ntchito m’dera la Nunavut ndiponso m’dera la kumpoto cha kum’mwera kwa dzikoli.

Mayi Velma Illasiak, omwe ndi mphunzitsi wamkulu pa sukulu inayake m’dera la Aklavik analankhulapo zokhudza ntchito yapadera imene a Mboni ankagwira m’deralo. Iwo anati: “Ana asukulu akusangalala kwambiri ndi uthenga umene mwawauza ndipo zawachititsa kuyamba kuganizira mozama za uthenga wa m’Baibulo . . . Moti tikuganiza zoitanitsa mabuku onse awiri a Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa.Tikuthokoza kwambiri kuti munabwera pasukulu yathu ino ndiponso m’dera lino.”

Bambo Peter Iyaituk, omwe ndi woyang’anira tauni ya Ivujivik kumpoto kwa dera la Quebec, analankhulana ndi a Mboni omwe ankalalikira m’derali ndiponso anaonera vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? Kenako bambowa ananyamula a Mboniwo pagalimoto yawo n’kumawaonetsa malo osiyanasiyana m’derali. Tsiku lomwe a Mboniwo ankachoka m’derali, bambowo anaperekeza a Mboniwo pagalimoto yawo kubwalo la ndege ndipo anawathokoza kwambiri chifukwa cha ntchito yomwe anagwira.

David Creamore yemwe ndi wa Mboni za Yehova akuonetsa vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? kwa bambo Peter Iyaituk omwe ndi woyang’anira tauni ya Ivujivik.

Bambo Matthieu Rozon, omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Canada anati: “A Mboni za Yehova amasangalala kuphunzitsa anthu Baibulo kwaulere. Moti anthu amene anagwira nawo ntchitoyi sanataye nthawi ndiponso mphamvu zawo pothandiza anthuwo.”

Pa miyezi iwiri imene a Mboni anagwira ntchito yapaderayi, anagawira mabuku ndiponso zinthu zina zokwana 37,000. Anthu pafupifupi 600 anapempha kuti a Mboniwo adzawayenderenso n’cholinga choti adzapitirize kukambirana mfundo za m’Baibulo.

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Canada: Matthieu Rozon, tel. +905 873 4100

Bwalo la Ndege la Kuujjuarapik ku Quebec

Kagulu ka a Mboni za Yehova kafika ku tauni ya Kuujjuarapik yomwe ili kum’mawa kwa doko la Hudson Bay.

Dera la Salluit ku Quebec

Dera la Salluit lili kumpoto kwa chigawo cha Quebec ndipo kuli anthu oposa 1,300.

Tauni ya Ivujivik ku Quebec

Tauni ya Ivujivik ili kumpoto kwa chigawo cha Quebec ndipo kuli anthu pafupifupi 400.

Tauni ya Ivujivik ku Quebec

Woyang’anira tauni ya Ivujivik, bambo Peter Iyaituk anyamula a David Creamore pagalimoto yawo kuti aone malo osiyanasiyana m’tauniyi.

Tauni ya Ivujivik ku Quebec

Mtsikana wolankhula Chiinukituti akuonera vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?

Dera la Paulatuk ku Zigawo za Kumpoto Chakumadzulo

Nyumba zinamangidwa mpaka m’mbali mwa nyanja ya Beaufort, m’dera lomwe ndi laling’ono kwambiri la anthu pafupifupi 300.

Tauni ya Umiujaq ku Quebec

A Julien Pinard omwe ndi a Mboni za Yehova akulandiridwa ndi banja lolankhula Chiinukituti kuti akambirane mfundo za m’Baibulo. Tauniyi ili ndi anthu pafupifupi 450.

Tauni ya Umiujaq ku Quebec

Anthu a m’tauniyi akujambulitsa chithunzi ndi a Roxanne Pinard omwe ndi a Mboni za Yehova.

Mudzi wa Puvirnituq ku Quebec

Muli anthu pafupifupi 1,700 ndipo uli kumpoto kwa Quebec.