Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

FEBRUARY 15, 2013
AUSTRALIA

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Australia

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Australia

SYDNEY—Madzi osefukira anamiza madera a kum’mwera kwa dziko la Australia. Kusefukira kwa madziku kunayamba chifukwa cha mphepo ya mkuntho yotchedwa Tropical Cyclone Oswald yomwe inayambitsa chimvula champhamvu m’mdera la Queensland ndi la kumpoto kwa New South Wales. Anthu 4 anafa ndipo oposa 1,000 anasowa malo okhala. Mzinda wa Bundaberg, womwe uli pakati pa chigawo chapafupi ndi nyanja cha Queensland, unawonongeka kwambiri chifukwa kunali kutachitika mphepo za mkuntho maulendo 5 madziwa asanasefukire.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Sydney inapereka lipoti lakuti palibe munthu wa Mboni amene anafa kapena kuvulala pa ngoziyi. Komabe nyumba 53 za anthu a Mboni za Yehova a ku Bundaberg zinawonongeka, ndipo izi zinachititsa kuti anthu 70 asowe pokhala. Anthu omwe nyumba zawo zinawonongekawa, omwe ena anachita kupulumutsidwa ndi ndege, akukhala m’nyumba za anthu oyandikana nawo kapena a Mboni za Yehova anzawo.

Akulu a mpingo wa Mboni za Yehova a m’derali anakhazikitsa komiti yopereka chithandizo kuti ithandize anthu okhudzidwa. Anthu 250 a Mboni za Yehova omwe ena anachokera kutali kwambiri anapita kuchigawo cha Bundaberg kuti akathandize anthu amene anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madziku.

Mukafuna kuimba foni:

Kuchokera m’mayiko ena: Lankhulani ndi a J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Kuchokera ku dziko lomweli la Australia: Lankhulani ndi a Donald MacLean, tel. +61 2 9829 5600