Pa November 12, 2013, dziko la Armenia linatulutsa m’ndende anthu onse a Mboni za Yehova omwe anamangidwa atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Vidiyoyi ikusonyeza zimene zinachitika pa mlanduwu mpaka pamene anthu a Mboniwa anatulutsidwa m’ndende.