Pitani ku nkhani yake

7 MAY, 2015
ANGOLA

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Madzi Osefukira ku Angola

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Madzi Osefukira ku Angola

Nyumba ya Ufumu ya a Mboni za Yehova ya ku Lobito yomwe inawonongeka ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi.

LUANDA, Angola—Kuyambira pa 11 March, 2015, mvula yodetsa nkhawa inagwa m’chigawo cha Benguela, chomwe chili pamtunda wa makilomita 500 kukafika mumzinda wa Luanda omwe ndi likulu la dzikoli. Mvulayi inachititsa kuti madzi asefukire ndipo madziwo anapha anthu 85 komanso kuononga nyumba 119. Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Angola inanena kuti palibe wa Mboni amene anamwalira. Komabe nyumba za a Mboni 11 zinawonongeka ndipo zina zinagweratu. M’dera la Lobito, Nyumba ya Ufumu, yomwe ndi malo amene a Mboni amasonkhanamo, inawonongekanso.

Madziwo atangosefukira, a Mboni za Yehova anakhazikitsa komiti yoti ifufuze ndi kuthandiza anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi. A Mboniwo ankathandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena omwe si a Mboni omwe ankakhala m’dera limene linasefukira madzi. A Mboni ena a m’derali anadzipereka kuti akonze Nyumba ya Ufumu ya ku Lobito ndipo anachotsa matope komanso madzi omwe analowa m’Nyumba ya Ufumuyo. Anachita zimenezi chifukwa ankafuna kuti adzachitiremo misonkhano yapadera yomwe inkayenera kuchitika kumapeto kwa mlungu. Oimira ofesi ya Mboni za Yehova m’dzikoli, anapita kuderali ndipo cholinga chawo chinali kukatonthoza komanso kukalimbikitsa a Mboni anzawo omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi.

A Mboni omwe anadzipereka kuchotsa matope ndi madzi omwe analowa mu Nyumba ya Ufumu ya ku Lobito.

Wolankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Angola, dzina lake Todd Peckham, anati: “Tikupepesa anthu onse amene anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madziku. Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Angola ipitirizabe kuyang’anira ntchito yothandiza anthu amenewa.”

Yankhulani Ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Angola: Todd Peckham, tel. +244 222 460 192