Pitani ku nkhani yake

FEBRUARY 17, 2014
PHILIPPINES

Nkhani Mwachidule: A Mboni za Yehova Akonza Ntchito Yothandiza Anthu Amene Anakhudzidwa ndi Mvula Yamkuntho ya Haiyan

Nkhani Mwachidule: A Mboni za Yehova Akonza Ntchito Yothandiza Anthu Amene Anakhudzidwa ndi Mvula Yamkuntho ya Haiyan

MANILA, Philippines—Pofuna kuthandiza kukonza zinthu zambiri zimene zinawonongedwa ndi mvula yamkuntho ya Haiyan, a Mboni za Yehova anakonza zoti athandize anthu amene anakhudzidwa tsokali, monga mmene amachitira m’mayiko ena.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Manila inakonza kuti pakhale makomiti 5 othandiza anthu n’cholinga choti ntchitoyi ichitike mofulumira. Katundu wothandizira anthu wokwana matani 190, wakhala akutumizidwa kuchigawo chapakati cha dziko la Philippines. Anthu a Mboni za Yehova ongodzipereka ochokera m’mayiko okwana 10 anagwira nawo ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi ngoziyi. Anthu ongodziperekawa anathandiza kukonza nyumba zimene zinawonongeka zokwana 2,000 ndiponso anapereka thandizo la mankhwala kwa anthu.

Anthu 225 akukhalabe m’matenti amene a Mboni anakonza kudera limene anasamutsirako anthu pafupi ndi mzinda wa Calbayog m’dera la Samar. Anthu 15 kapena 20 pa anthu 100 alionse amene akukhala pamalowa si a Mboni za Yehova.

Zikuonetsa kuti mvula yamkunthoyo inaposa ngozi zina zonse zachilengedwe zimene zakhala zikuchitika m’mbuyomu. Izi zili choncho chifukwa anthu 6,201 anafa pa ngoziyi komanso ena 1,785 akusowabe. Anthu 28,000 anavulala ndiponso nyumba 1 miliyoni zinawonongedwa. Akuluakulu aku ofesi ya Mboni za Yehova ku Philippines yomwe ili mumzinda wa Manila, anatsimikizira kuti anthu a Mboni 33 anaphedwa ndipo ena 10 akusowa kapena kuganiziridwa kuti anafa ndi ngoziyi.

A Mark Sanderson, a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova akuyendera anthu amene anakhudzidwa ndi mvula yamkuntho.

Kuyambira pa December 7, 2013, a Mark Sanderson omwe ndi a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anayendera madera 5 amene anakhudzidwa ndi ngoziyi kwa masiku 7. Iwo anafotokoza kuti: “Mvula yamkuntho ya Haiyan inabweretsa mavuto ochuluka kwa anthu ambiri ku Philippines. Komabe tiyesetsa kupitiriza kuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi powapatsa zinthu zofunikira. Tionetsetsa kuti pali anthu amene akuwathandiza komanso kuwalimbikitsa kuti zinthu ziyambenso kuwayendera.

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Philippines: Dean Jacek, tel. +63 2 411 6090