Pitani ku nkhani yake

JULY 3, 2014
MEXICO

A Mboni Anachita Nawo Chionetsero cha Mabuku ndi Magazini Mumzinda wa Mexico City

A Mboni Anachita Nawo Chionetsero cha Mabuku ndi Magazini Mumzinda wa Mexico City

MEXICO CITY—A Mboni za Yehova anali nawo pagulu la makampani 150 ofalitsa mabuku omwe anachita chionetsero cha mabuku ndi magazini. Aka ndi koyamba kuti chionetsero chotere chichitike. Chionetserochi chinakonzedwa ndi bungwe loona za ntchito zolemba ndi kufalitsa mabuku m’dziko la Mexico la National Chamber for the Mexican Publishing Industry (CANIEM). Chionetserochi chinachitika kuyambira pa April 25 mpaka pa May 4, 2014 ku Likulu la Zamalonda Padziko Lonse lomwe lili mumzinda wotchedwa Mexico City. Anachita chionetserochi pokumbukira kuti bungwe loona za ntchito zolemba ndi kufalitsa mabuku m’dziko la Mexico latha zaka 50 ndipo anthu pafupifupi 20,000 anapezeka pa chionetserochi.

A Mboni anaika pamashelefu mabuku, magazini komanso mavidiyo osiyanasiyana ofotokoza nkhani za m’Baibulo. Anasonyezanso webusaiti yawo yovomerezeka ya www.jw.org, pomwe pali mabuku ndi zinthu zina zomwe anthu akhoza kupanga dawunilodi zomwenso zikupezeka m’zinenero zoposa 650. Anthu omwe anafika pamalowa anatenga mabuku ndi zinthu zina zoposa 1,600 kwa a Mboni ndipo ena anapempha a Mboniwa kuti adzakakambirane nawo nkhani za m’Baibulo kunyumba kwawo. Monga mmene a Mboni za Yehova amachitira nthawi zonse, mabuku ndi magazini zinali zaulere chimodzimodzinso ndi kuphunzira Baibulo ndi anthu kunyumba zawo.

Bambo Gamaliel Camarillo, omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Mexico, anati: “Tinasangalala kwambiri kuti anthu ambirimbiri ankabwera pamene panali mashelefu athu, ndipo ankachita chidwi ndi nkhani za m’Baibulo komanso webusaiti yathu ya jw.org. Tikuona kuti tinathandiza anthu popititsa mabuku ndi zinthu zina zomwe ndi zothandiza kwambiri kwa anthu, n’kumawapatsa kwaulere akapempha. Ndi mwayi waukulu kuti tinachita nawo chionetserochi.”

Kuchokera m’mayiko ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Mexico: Gamaliel Camarillo, tel. +52 555 133 3048