Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 28, 2014
MEXICO

A Mboni za Yehova ku Mexico Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Mphepo ya Mkuntho ya Hurricane Odile

A Mboni za Yehova ku Mexico Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Mphepo ya Mkuntho ya Hurricane Odile

Mphepo yamkuntho yotchedwa Hurricane Odile inawononga nyumba komanso katundu wa anthu ambiri pachilumba cha Baja California Sur. Izi zinachitika Lolemba pa September 15, 2014, ndipo a Mboni za Yehova amene amakhala kufupi ndi derali, anabwera ndi chakudya, madzi komanso mankhwala kuti zithandize a Mboni omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi. Palibe wa Mboni amene anamwalira kapena kuvulala pa mphepo yamkuntho yamphamvu kwambiri imene inaomba pachilumbachi. Mphepo yofanana ndi imeneyi inaombanso pachilumbachi mu 1967. Komabe, mphepoyi inagwetsa nyumba 82 za a Mboni ndipo nyumba 85 zinawonongeka kwambiri. Izi zinachititsa kuti mabanja a Mboni 125 asowe pokhala. Koma n’zosangalatsa kuti a Mboni ena anapereka nyumba kwa abale awowo kuti azikhala. Kutatsala masiku 4 kuti mphepoyi ichitike, makomiti a Mboni othandiza pakachitika tsoka anatumiza makalata m’mipingo ya Mboni za Yehova ya m’derali ofotokoza zimene angachite pokonzekera ngoziyi. Akulu a m’mipingoyo anakonza zoti a Mboni omwe amakhala m’nyumba zosalimba achoke n’kumakakhala m’nyumba za a Mboni anzawo. Pofuna kuthandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyo, ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Mexico inatumiza zinthu zosiyanasiyana zolemera matani 20 ku derali.

Kuchokera M’mayiko Ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Mexico: Gamaliel Camarillo, tel. +52 555 133 3048