Pitani ku nkhani yake

MAY 22, 2015
MEXICO

A Mboni za Yehova Anachita Nawo Chionetsero Chachikulu cha Mabuku a Chisipanishi

A Mboni za Yehova Anachita Nawo Chionetsero Chachikulu cha Mabuku a Chisipanishi

MEXICO CITY—A Mboni za Yehova anaitanidwa kuti akachite nawo chionetsero cha padziko lonse cha mabuku a Chisipanishi ku Guadalajara. Chionetserochi chinali chachikulu kwambiri pa zionetsero zonse zimene zinachitikapo m’mayiko olankhula Chisipanishi ndipo chinali chachiwiri pa zionetsero zonse za mabuku zimene zachitikapo padziko lonse. Chionetsero chachikulu kwambiri padziko lonse chinachitika ku Frankfurt m’dziko la Germany. Anthu oposa 760,000 ndi amene anafika pa chionetsero cha ku Mexico chomwe chinachitika pa November 28 mpaka December 6, 2014.

Mabuku a Zimene Achinyamata Amadzifunsa oposa 4,000 anagawidwa kwa anthu.

Pa chionetserochi panafika magulu ofalitsa mabuku okwana 1,900 ochokera m’mayiko 44. Pamwambowu a Mboni anakonza kanyumba komwe anaikamo Mabaibulo ndiponso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Ena mwa mabukuwa ali ndi mfundo zothandiza mabanja, achinyamata ndiponso ana.

Bambo Gamaliel Camarillo, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Mexico, ananena kuti: “Pamasiku 4 amene tinaonetsa mabuku athu, anthu oposa 10,000 anafika pamalo athu ndipo tinagawa mabuku pafupifupi 29,000 kwaulere. Koma cholinga chathu sikungogawa mabuku. Magazini komanso mabuku athu ali ndi mfundo za m’Baibulo zimene zimathandiza anthu mamiliyoni ambiri pamoyo wawo.”

Lankhulani Ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Mexico: Gamaliel Camarillo, tel. +52 555 133 3048