Pitani ku nkhani yake

Malo Othandiza Atolankhani

UKRAINE

A Mboni Anaulutsa Msonkhano Wapadera Kudera Limene Kunali Nkhondo ku Ukraine

A Mboni za Yehova a ku Ukraine anakhala ndi msonkhano wapadera pa 14 February 2015 kuti alimbikitse Akhristu anzawo oposa 17,000 omwe ali m’dera limene kunali nkhondo.

NEPAL

A Mboni za Yehova Akuthandiza Anthu Okhudzidwa ndi Chivomerezi ku Nepal

A Mboni za Yehova ochokera ku mayiko 6 limodzi ndi komiti ya ku Nepal yopereka chithandizo pakagwa zamwadzidzidzi akuthandizabe anthu powapatsa zofunika pa moyo ndiponso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.

MEXICO

A Mboni za Yehova Anachita Nawo Chionetsero Chachikulu cha Mabuku a Chisipanishi

Pa chionetsero cha mabuku ku Guadalajara panaonetsedwa mabuku amene anthu amalemba kuzungulira dziko lonse ndiponso mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

UNITED STATES

A Mboni za Yehova Ayamba Misonkhano Yachigawo ya Mutu Wakuti “Tsanzira Yesu,” M’mizinda 11 ku United States

Misonkhanoyi iyamba mlungu uno ku California, Hawaii, Maine, Massachusetts, New Jersey, New York, Oregon ndi ku Wisconsin. Pachitika misonkhano pafupifupi 5,000 m’madera 92 ndipo ikhala ikuchitika mpaka mu January 2016.

CHILE

A Mboni Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Madzi Osefukira ku Chile

Madzi atangosefukira ku Chile a Mboni anayamba kuthandiza anthu.

UNITED STATES

A Mboni za Yehova Atsegulira Ofesi Yomasulira Chinenero Chamanja cha ku America Kudera la Florida

A Mboni za Yehova anasamutsa ntchito yomasulira mabuku m’chinenero chamanja cha ku America mumzinda wa Fort Lauderdale ku Florida m’dziko la United States. Anachita zimenezi chifukwa mumzindawu muli anthu ochokera kosiyanasiyana omwe amagwiritsa ntchito chinenero chamanja cha ku America.

ANGOLA

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Madzi Osefukira ku Angola

Madzi atangosefukira m’chigawo cha Benguela ku Angola, a Mboni anakhazikitsa komiti yoti ithandize anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi.

GUATEMALA

Sukulu za ku Guatemala Zinapempha Mabuku kwa a Mboni za Yehova Pofuna Kuthandiza Achinyamata Kuti Asiye Kuchita Zachiwawa

Sukulu za ku Guatemala zinapempha mabuku athu ambiri omwe ndi a zinenero za Chispanish komanso Quiché. Mabukuwa amawagwiritsa ntchito pophunzitsa m’kalasi n’cholinga chofuna kuthandiza ana a sukulu kuti akhale ndi makhalidwe abwino.

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Alengeza za Misonkhano Yachigawo ya 2015

Misonkhano yachigawo ya 2015 ya Mboni za Yehova ya mutu wakuti “Tsanzirani Yesu” idzathandiza anthu kudziwa mmene angapindulire ndi chitsanzo cha Yesu. Misonkhanoyi idzachitika m’madera osiyanasiyana padziko lonse kuyambira mu May 2015 mpaka January 2016.

MEXICO

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chinenero cha Chitsotsilu Linatulutsidwa ku Mexico

A Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu (Chipangano Chatsopano) la Chinenero cha Chitsotsilu. Chinenerochi chimayankhulidwa ndi anthu a mtundu wa Maya omwe amakhala m’madera okwera a chigawo chapakati ku Chiapas.

RUSSIA

Wa Mboni Wina wa ku Russia Anatola Ndalama Zokwana Mayuro 6,000 Ndipo Anazibweza kwa Mwini Wake

Mayi Svetlana Nemchinova, omwe ndi a Mboni za Yehova, anafufuza mwini wa ndalama zomwe zinatayidwa mwangozi pamalo ena.

VANUATU

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho

A Mboni za Yehova akuthandiza komanso kulimbikitsa anthu amene katundu wawo kapena nyumba zawo zinawonongeka ndi mphepo yoopsa.

MOZAMBIQUE

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Mozambique

A Mboni za Yehova akupitiriza kupereka zinthu zofunika kwa anthu okhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi m’chigawo chakumpoto ndi chapakati m’dziko la Mozambique. Kuwonjezera pamenepa, akuwalimbikitsanso pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

UNITED STATES

A Mboni Analandira Mphoto Chifukwa Chosamalira Zachilengedwe pa Ntchito Yawo Yomanga

Nyumba ziwiri zomwe zinamangidwa ndi a Mboni za Yehova ku Wallkill mumzinda wa New York, zinalandira mphoto chifukwa chomangidwa mosawononga chilengedwe.

KAZAKHSTAN

A Mboni za Yehova Anagawa Baibulo la Chinenero cha Chikazaki Pamsonkhano Komanso Pamwambo Umene Anaitanira Anthu Ambiri

A Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Chikazaki pamsonkhano womwe unachitikira munzinda wa Almaty ku Kazakhstan.