Pitani ku nkhani yake

Malo Othandiza Atolankhani

RUSSIA

Akuluakulu a Boma la Russia Akufuna Kutseka Likulu la Mboni za Yehova M’dzikolo

Kalata imene akuluakulu a boma la Russia alemba posachedwapa ikusonyeza kuti bomali likufuna kuletsa a Mboni kupembedza.

HUNGARY

Pamalo Osungirako Mbiri Yokhudza Nkhanza za Chipani cha Nazi ku Hungary Panaonetsedwa Chithunzi Cholemekeza a Mboni Amene Anaphedwa

Pofuna kukumbukira a Mboni za Yehova 4 amene anaphedwa chifukwa chokana kuchita zinthu zosagwirizana ndi chikumbumtima chawo panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, Pamalo Osungira Mbiri Yokhudza Nkhanza za Chipani cha Nazi panaonetsedwa chithunzi cha Amboniwo.

RUSSIA

Komiti Ina ya Bungwe la United Nations Yanena Kuti Dziko la Russia Likugwiritsa Ntchito Lamulo Loteteza Anthu ku Zinthu Zoopsa Polimbana ndi a Mboni

Komiti Ina ya Bungwe la United Nations Yanena Kuti Dziko la Russia Likugwiritsa Ntchito Lamulo Loteteza Anthu ku Zinthu Zoopsa Polimbana ndi a Mboni

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Padziko Lonse Ayamba Kugwira Ntchito Yoitanira Anthu ku Mwambo Wapachaka Wokumbukira Imfa ya Yesu

A Mboni za Yehova padziko lonse ayamba kugwira ntchito yoitanira anthu ku mwambo wapachaka wokumbukira imfa ya Yesu womwe udzachitike pa 23 March, 2016.

UNITED STATES

A Mboni za Yehova Amaliza Kumanga Mbali Yaikulu ya Likulu Lawo Latsopano Lapadziko Lonse

A Mboni za Yehova akuyembekezera kuti pofika pa 1 September, 2016, amaliza ntchito yomanga likulu lawo latsopano lapadziko lonse.

UNITED STATES

A Mboni Ayamba Kugulitsa Nyumba Zawo za ku Brooklyn

A Mboni za Yehova akugulitsa nyumba zawo zomwe anthu ambiri akhala akuzifuna ndipo nyumbazi zili m’dera la Dumbo ndiponso Brooklyn Heights mumzinda wa New York.

MEXICO

Boma Linathokoza a Mboni Chifukwa Chophunzitsa Akaidi ku Mexico

Akuluakulu a boma anathokoza Mboni za Yehova chifukwa chophunzitsa Baibulo akaidi a m’ndende za ku Baja California.

GHANA

A Mboni za Yehova Anathandiza ku Ghana Kutasefukira Madzi

Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Ghana inakhazikitsa komiti yomwe cholinga chake chinali kukathandiza anthu ndipo inapereka madzi komanso thandizo la mankhwala kwa anthu amene anakhudzidwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi.

RUSSIA

Akatswiri Ena Sanagwirizane ndi Zimene Dziko la Russia Lachita Poletsa JW.ORG

Pa 21 July 2015 dziko la Russia linaletsa webusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova ya jw.org ndipo dzikoli ndi loyamba kuchita zimenezi.

AUSTRIA

Chikwangwani Chachikumbutso Chinaikidwa Pokumbukira wa Mboni Amene Anaphedwa ndi a Chipani cha Nazi

Gabriele Votava ndi amene anali mlendo wolemekezeka pamwambo wokumbukira Gerhard Steinacher, yemwe anali wa Mboni za Yehova ndipo anaphedwa ali ndi zaka 19 chifukwa chokana kulowa usilikali.

CANADA

Akuluakulu a Boma Kumpoto kwa Dziko la Canada Anayamikira a Mboni za Yehova Chifukwa cha Ntchito Yawo Yophunzitsa Baibulo

A Mboni za Yehova analalikira madera akutali kuchokera ku Aklavik, zigawo za kumpoto chakumadzulo, ku Kangiqsualujjuaq ndiponso cha kum’mawa ku Quebec.

ZIMBABWE

Misonkhano ya Chaka cha 2015 ya Mboni za Yehova Yakuti “Tsanzirani Yesu” Yayamba Kuchitika ku Zimbabwe Patatha Chaka Chimodzi Kuchokera Pamene Kunachitika Msonkhano wa Mayiko

Msonkhano wa mayiko womwe unachitika mu 2014 ku Zimbabwe unali wosaiwalika ndipo unapangitsa kuti akhale ndi chidwi pa msonkhano wa chaka chino.

GERMANY

Bambo Wina ndi Mwana Wake Analandira Mendulo Yaulemu Chifukwa Chopulumutsa Anthu pa Ngozi ya Galimoto

A Andreas Bonk, omwe ndi a Mboni za Yehova, ndi mwana wawo Jorim analandira mendulo yaulemu chifukwa chakuti anachita zinthu molimba mtima komanso mosaganizira moyo wawo.