Pitani ku nkhani yake

Malo Othandiza Atolankhani

COLOMBIA

A Mboni Anapatsidwa Mphoto ndi Bungwe Loona Ntchito Yomasulira M’chinenero cha Manja ku Colombia

A Mboni za Yehova ku Colombia analandira mphoto ziwiri powayamikira chifukwa cha ntchito yawo yomasulira m’Chinenero Chamanja cha ku Colombia.

UNITED STATES

A Mboni Akukonzanso Damu ku Warwick Lomwe Lakhala kwa Zaka 60

A Mboni za Yehova anakonzanso damu la Blue Lake lomwe lili mkatikati mwa nkhalango ya Sterling Forest State Park pamene ankamanga likulu lawo latsopano.

UNITED STATES

A Mboni akugulitsa nyumba yawo ya ku 97 Columbia Heights

Pa 26 October, 2016, a Mboni za Yehova analengeza kuti akugulitsa nyumba yawo ya ku 97 Columbia Heights yomwe poyamba inkadziwika kuti Hotel Margaret.

ITALY

A Mboni za Yehova Analimbikitsa Anthu Amene Anakhudzidwa ndi Chivomerezi ku Italy

Pa ntchito yapadera yomwe inachitika padziko lonse, a Mboni za Yehova ku Italy analalikira uthenga wolimbikitsa anthu omwe anakhudzidwa ndi chivomerezi m’madera a Lazio, Marche ndi Umbria.

RUSSIA

Zimene Akatswiri Ena Ananena: Dziko la Russia Likugwiritsa Ntchito Molakwika Lamulo Loteteza Anthu ku Zinthu Zoopsa Pofuna Kuletsa Ntchito ya Mboni za Yehova

Iyi ndi nkhani yoyamba pa nkhani zitatu zochokera pa zimene a katswiri pa nkhani ya zipembedzo, ndale, chikhalidwe komanso akatswiri a ulamuliro wa Soviet ananena.

UNITED STATES

A Mboni za Yehova Agulitsa Nyumba Zimene Zinali Likulu Lawo ku Brooklyn

Pa 3 August, 2016, a Mboni za Yehova anagulitsa nyumba zawo zomwe zinali likulu lawo padziko lonse. Nyumbazi zili ku 25/30 Columbia Heights ku Brooklyn, mumzinda wa New York

SRI LANKA

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu M’dziko la Sri Lanka Mutagwa Chimvula Choopsa

Patangodutsa zaka 12 kuchokera pamene ku Sri Lanka kunachitika tsunami, m’dzikoli munachitikanso ngozi ina ndipo a Mboni za Yehova anathandiza anthu omwe anakhudzidwa.

UNITED STATES

A Mboni za Yehova Akugulitsa Nyumba Imene Inali Chuma Chawo Chapadera ku Brooklyn Yotchedwa The Towers

Pa 24 May, 2016 a Mboni za Yehova anaika nyumba yawo yotchedwa The Towers yomwe ili mu mzinda wa Brooklyn pa mndandanda wa nyumba zimene akugulitsa.

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya  2016 Ikufotokoza za Kukhala Okhulupirika

A Mboni za Yehova adzachita Misonkhano ya 2016 yamutu wakuti “Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova” m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse. Aliyense akuitanidwa ku msonkhanowu womwe udzachitike kwa masiku atatu kwaulele.