Pitani ku nkhani yake

Malo Othandiza Atolankhani

ITALY

Msonkhano Wofunika Kwambiri Wokambirana Zimene Zachitika pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi Unachitikira ku Yunivesite ya Padua

Anthu akhala akukhulupirira kuti kuika munthu magazi kulibe vuto lililonse ndipo ndi njira yokhayo yopulumutsira moyo wa anthu omwe adwala kwambiri kapena omwe akufunika kupangidwa opaleshoni. Koma anthu ambiri omwe anayankhula pamsonkhanowu, sanagwirizane ndi maganizo amenewa.

ITALY

Kufunsa a Pulofesa Antonio D. Pinna, M.D.

“Ndikuganiza kuti kukana magazi chifukwa cha chipembedzo si vuto. Palinso odwala ena amene safuna kuikidwa magazi koma si a Mboni.”

RUSSIA

Akuluakulu a Boma ku Russia Akufuna Kulanda Malo ndi Nyumba za Bungwe la Mboni za Yehova la ku America

Mlandu wa apilo uyamba ku khoti la mu mzinda wa Saint Petersburg pa nkhani yofuna kulanda ofesi yakale ya Mboni za Yehova ku Russia.

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya 2018 Iyamba mu May

Misonkhanoyi isanayambe, a Mboni padziko lonse azigwira ntchito yoitanira anthu kuti adzapezeke nawo pa misonkhanoyi yomwe ndi yaulere.

ISRAEL

Chionetsero Chomwe Chinachitika ku Tel Aviv Chinasonyeza Mavuto Omwe a Mboni za Yehova Anakumana Nawo mu Ulamuliro wa Nazi

Chionetsero chomwe chinachitikira ku Hatachana chinakonzedwa kuti chithandize anthu kudziwa nkhanza zimene a Mboni za Yehova anakumana nazo mu ulamuliro wa chipani cha Nazi.

AUSTRIA

Akuluakulu a Tauni Ina ku Austria Anachita Mwambo Wokumbukira a Mboni 31 Omwe Anazunzidwa Komanso Kuphedwa mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi

Chikwangwani cha ku Techelsberg chinakonzedwa pokumbukira a Mboni za Yehova omwe anazunzidwa ndi a chipani cha Nazi pa nthawi ya Nkhondo Yachiwiri ya Padziko Lonse.

RUSSIA

Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia Lagamula Kuti Likulu la Mboni za Yehova M’dzikolo Litsekedwe

A Mboni apanga apilo pa zimene khoti lagamula kuti likulu lawo m’dziko la Russia litsekedwe.

RUSSIA

A Mboni za Yehova Apereka Umboni Patsiku Lachitatu la Mlandu ku Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia

A Mboni 4 anafotokoza mfundo zofunika kwambiri zotsutsa zimene a Unduna wa Zachilungamo ananena zokhudza a Mboni m’dzikolo.

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Akukonzekera Misonkhano Ikuluikulu M’chaka cha 2017

A Mboni akugwira mwakhama ntchito yoitanira anthu ku misonkhano yawo ikuluikulu ya pachaka, ndipo msonkhano woyamba udzakhala wokumbukira imfa ya Yesu.

THAILAND

Akuluakulu a Boma la Thailand Akugwiritsa Ntchito Mabuku a Mboni za Yehova Pothandiza Anthu a M’dziko Lawo

Kwa zaka zitatu zapitazi, akuluakulu a boma ku Thailand akhala akugwiritsa ntchito mabuku a Mboni pophunzitsa anthu makhalidwe abwino.