Pitani ku nkhani yake

Malo Othandiza Atolankhani

GERMANY

Dziko la Germany Lapereka Mendulo Yaulemu kwa Mayi Wina wa Mboni za Yehova Poyamikira Ntchito Yake Yotamandika

Mathilde Hartl analandira mendulo yaulemu imene boma la Germany limapereka kwa anthu okhawo amene achita zinthu zazikulu. Anapereka menduloyi ndi nduna yaikulu ya chigawo cha Bavaria.

AUSTRALIA

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Australia

Mphepo yotchedwa Tropical Cyclone Oswald inayambitsa mvula yamphamvu ku Australia. A Mboni za Yehova a m’derali anakhazikitsa komiti yopereka chithandizo kuti ithandize anthu okhudzidwa.

ARMENIA

Khoti Lalamula Dziko la Armenia Kuti Lipereke Chipukuta Misozi kwa Anthu 17 a Mboni za Yehova

Pa November 27, 2012, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linalamula dziko la Armenia kuti lipereke chipukuta misozi cha ndalama zokwana madola 145,226 kwa anthu 17 chifukwa chowaphwanyira ufulu. Anthuwa anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

UNITED STATES

Kavidiyo: Ku Manhattan Kwayambika Ntchito Yapadera

A Mboni za Yehova ku Manhattan mumzinda wa New York, ayambitsa ntchito yapadera yogawira mabuku awo ofotokoza nkhani za m’Baibulo a m’zinenero zosiyanasiyana. Iwo akumaika mabukuwo pamatebulo omwe akumawaika m’malo osiyanasiyana ku Grand Central Station. Kodi anthu akunena zotani?

JAPAN

Timavidiyo: Japan: Moyo ukuyambiranso ku Japan patapita chaka chimodzi chivomezi chitachitika

Anthu a Mboni za Yehova akupitiriza kuthandiza anthu amene anapulumuka kutachitika chivomezi ndi madzi osefukira.

RUSSIA

Mavuto Amene a Mboni Akhala Akukumana Nawo kwa Zaka 10 pa Nkhani Zamalamulo Anaunikidwa pa Tsiku la 5 Lozenga Mlandu ku Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia

Maloya oimira Unduna wa Zachilungamo sanathe kunena chifukwa chomveka chokhudza malamulo chochititsa kuti Likulu la Mboni za Yehova litsekedwe ku Russia.

RUSSIA

Akatswiri Ena Akana Kuti Boma la Russia Liletse Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Nkhaniyi ndi yachiwiri pa nkhani zitatu zomwe zikufotokoza zimene ananena akatswiri a zachipembedzo, a zandale, zachikhalidwe cha anthu komanso a maphunziro a ulamuliro wa Soviet Union.

HAITI

Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudziwa ndi Mphepo Yoopsa Yotchedwa Matthew ku Haiti Yatsala Pang’ono Kutha

Ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi ikuyembekezereka kutha pofika mu June 2017.

MALAWI

Ana Awiri a Mboni za Yehova Anawalola Kuyambiranso Sukulu Atawachotsa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Ana awiri a Mboni za Yehova anawachotsa sukulu chifukwa chokana kuimba nawo nyimbo ya fuko. Akuluakulu a pasukulupo anawalola kuti ayambirenso sukulu.

RUSSIA

Pulezidenti Putin Anapereka Mphoto kwa Makolo a Mboni za Yehova Chifuwa Cholera Bwino Ana Awo

Pa mwambo umene unachitikira kunyumba ya boma mumzinda wa Moscow, pulezidenti Vladimir Putin anapereka mphoto kwa a Valeriy ndi a Tatiana Novik, omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo amakhala ku Karelia.

UNITED KINGDOM

A Mboni Anapatsidwa Mphotho Yapamwamba Chifukwa Chogwiritsa Ntchito Njira Zamakono Pomanga Nthambi Yawo Yatsopano ku Britain

A Mboni za Yehova ku analandira mphoto yapamwamba chifukwa cha mmene anamangira nthambi yawo yatsopano ku Britain komanso chifukwa chogwiritsa ntchito njira zatsopano zoteteza chilengedwe pa ntchitoyi.