Vidiyo ya Mboni Yathandiza Makolo Kudziwa Zimene Angachite Kuti Athandize Ana Amene Amavutitsidwa ndi Anzawo
Vidiyo yaifupi yamakatuni yakuti Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani? Inapangidwa ndi a Mboni za Yehova, ndipo ili ndi malangizo othandiza achinyamata amene amavutitsidwa.
Vidiyo ya Mboni Yathandiza Makolo Kudziwa Zimene Angachite Kuti Athandize Ana Amene Amavutitsidwa ndi Anzawo
Vidiyo yaifupi yamakatuni yakuti Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani? Inapangidwa ndi a Mboni za Yehova, ndipo ili ndi malangizo othandiza achinyamata amene amavutitsidwa.
Akuluakulu a Boma ku Russia Anathokoza Mwapadera a Mboni za Yehova Kuphatikizapo Nzika ya ku Denmark Yomwe ili M’ndende
Akuluakulu mumzinda wa Oryol anathokoza a Mboni za Yehova kuphatikizapo nzika ina ya ku Denmark yomwe ili m’ndende. Iwo anathokoza Amboniwo chifukwa chogwira nawo ntchito yoyeretsa mumzindawo yomwe imachitika chaka chilichonse.
A Mboni za Yehova Akugwira Ntchito Yokonza Zinthu Zomwe Zinaonongeka ndi Mvula Yamkuntho Yotchedwa Nock-Ten
A Mboni za Yehova akugwira nawo ntchito yokonzanso ndi kumanga nyumba zambirimbiri zomwe zinaonongedwa kapena kugwa ndi mvula yamkuntho ku Philippines chakumapeto kwa 2016.
Akuluakulu a Boma ku Ukraine Anakaona Malo ku Ofesi ya Mboni za Yehova Patsiku Lapadera
Kwa nthawi yoyamba kuchokera mu 2001, ofesi ya mboni za Yehova ku Ukraine inakonza tsiku lapadera kuti anthu adzaone ntchito zimene zimachitika paofesiyo ndipo zimene zinachitika pa 2 May, 2017.
DEMOCRATIC REPUBLIC OF THE CONGO
A Mboni za Yehova Anapereka Chithandizo kwa Anthu Othawa Nkhondo ku Congo
A Mboni za Yehova akupereka chithandizo kwa Akhristu anzawo komanso anthu ena omwe anathawa nkhondo m’chigawo cha Kasai ku Democratic Republic of the Congo.
Tsiku Loona Malo ku Warwick: Kucheza ndi a Ingrid Magar
‘Ndasangalala kwambiri ndi ntchito imene yachitika ku Warwick. Zimene mwachita zapangitsa kuti malowa akhale okongola kwambiri. Ndikuona kuti ndi mwayi waukulu kukhala pafupi ndi anthu inu.’
Vidiyo Yosonyeza Apolisi ku Russia Akusokoneza Misonkhano ya Mboni za Yehova
Vidiyo yomwe bungwe lina lofalitsa nkhani ku Russia linatulutsa inasonyeza apolisi a Federal Security Service omwe anali ndi zida akusokoneza misonkhano imene a Mboni za Yehova ankapanga mumzinda wa Oryol ku Russia.
Vidiyo Yosonyeza Apolisi ku Russia Akusokoneza Misonkhano ya Mboni za Yehova
Pa 25 May 2017, apolisi a Federal Security Service (FSB) omwe anali ndi zida anasokoneza misonkhano imene a Mboni za Yehova ankachita mwamtendere mumzinda wa Oryol ku Russia.
A Mboni za Yehova Padziko Lonse Akulimbikitsidwa Kulemba Makalata Opempha Kuti Boma la Russia Lisaletse Ntchito Yawo M’dzikolo
Boma la Russia laopseza kuti liletsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. Choncho a Mboni za Yehova padziko lonse aganiza zolemba makalata opita ku boma la Russia ndiponso kwa akuluakulu a Khoti Lalikulu m’dzikolo. Pali malangizo omwe angathandize aliyense amene akufuna kulemba nawo makalatawa.
Pamene Chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri Chikuyandikira, Wokana Kulowa Usilikali Akuyembekezera Mwachidwi
Pa 30 August, 2018, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Korea lidzamva maganizo a anthu pa zimene Khoti Loona za Malamulo linagamula pa mlandu wa anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.
Kufunsa a Luca P. Weltert, M.D.
“Taona kuti pali kusintha kwakukulu chifukwa chochepetsa kugwiritsa ntchito magazi pothandiza odwala ndipo zimenezi sizinakhudze odwala a Mboni okha, koma zakhudzanso dziko lonse lapansi chifukwa pali maumboni ochuluka osonyeza kuti kuchepetsa kugwiritsa ntchito magazi kuli ndi zotsatira zabwino kwambiri.”