Pitani ku nkhani yake

AUGUST 28, 2015
UKRAINE

Khoti Lalikulu ku Ukrain Lagamula Kuti Anthu Ali ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali pa Zifukwa za Chipembedzo

Khoti Lalikulu ku Ukrain Lagamula Kuti Anthu Ali ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali pa Zifukwa za Chipembedzo

Khoti lalikulu ku Ukrain lagamula kuti anthu ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali ngakhale pa nthawi ya ziwawa za ndale kapena nkhondo. Chigamulochi chakhudza kwambiri nkhani za ufulu wachibadwidwe ku Ukrain ndiponso kumayiko ena.

Bambo Vitaliy Shalaiko, omwe ndi a Mboni za Yehova, anaimbidwa mlandu pa nthawi yomwe anapempha kuti m’malo molowa usilikali, agwire ntchito zina zosakhudzana ndi usilikaliwo. Khoti lomwe linkazenga mlanduwu ndiponso khoti la apilo linapeza kuti a Vitaliy Shalaiko alibe mlandu. Koma woimira boma pa mlanduwu anachita apilo ku khoti loona za milandu ikuluikulu. Pa 23 June, 2015, khotili linakana kuzenganso mlanduwu ndipo linagwirizanabe ndi chigamulo choyamba chija.

Khoti lalikulu linanena kuti: “Chigamulochi ndi cha chilungamo kwambiri chifukwa ndi mmene makhoti ena akuluakulu amaweruzira milandu ngati imeneyi.” Khotili linagwirizananso ndi zoti chigamulo cha mlanduwu chifanane ndi chigamulo chimene chinaperekedwa pa mlandu wa pakati pa a Bayatyan ndi dziko la Armenia. Chigamulo chokhudza mlandu wa a Bayatyan chinagamulidwa ndi Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya pa 7July, 2011. Ndipo chigamulochi chinasintha zinthu kwambiri pa nkhani ya ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha chipembedzo, zomwe n’zogwirizana ndi gawo 9 la Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Pa nkhani ya bambo Vitaliy Shalaiko yokhudza kukana kulowa usilikali, khoti lalikulu ku Ukrain linanena kuti ufulu wokana kulowa usilikali uyenera kutetezedwa ngakhale m’dziko mutachitika ziwawa za ndale kapena pamene boma likufuna kuti lilembe anthu ntchito ya usilikali.. Zimene khoti lalikululi lanena zikutsimikizira kuti chigamulo chokhudza mlanduwu sichingasinthe ndipo sipachitikanso apilo iliyonse.

Chigamulochi chinathandiza kwambiri kuti bambo Shalaiko asakhalenso ndi nkhawa. Bambowa ananena kuti: “Ndikudziwa kuti dziko lathu likufuna kuti anthu alowe usilikali kuti liteteze nzika zake. Ngakhale kuti sindingalowe usilikali chifukwa cha zimene ndimaphunzira m’Baibulo, ndine wokonzeka kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali pofuna kuthandiza dziko lathu. Ndine wosangalala kwambiri chifukwa makhoti azindikira kuti ndikukana kulowa usilikali pa zifukwa za chipembedzo.”

Chigamulochi Chithandiza Anthu Ambiri

A Mboni za Yehova ambirimbiri m’dziko la Ukrain akulimbana ndi nkhani yokana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira. Amene akuimbidwa mlandu wokana kulowa usilikali, tsopano athandizidwa kwambiri ndi chigamulo chimene chaperekedwa pa mlandu wa bambo Vitaliy Shalaiko.

Loya yemwe ankaimira a Shalaiko pa mlanduwu anali bambo Vadim Karpov, ndipo ananena kuti: “Kunena mosapita m’mbali, zimene khoti lalikulu lagamula zikusonyezeratu kuti, monga wa Mboni za Yehova, bambo Shalaiko sanayenera kuimbidwa mlandu chifukwa chokana kulowa usilikali. Ngakhale m’dziko la Ukrain momwe muli ziwawa za ndale, tiyenerabe kutsatira malamulo amene mayiko ena amayendera pa nkhani yolemekeza ufulu wachipembedzo ndiponso ufulu wotsatira zimene munthu amakhulupirira.”

Dziko la Ukrain Lasonyeza Chitsanzo Chabwino pa Nkhani Yolemekeza Ufulu Wachibadwidwe

Makhoti a ku Ukrain azindikira kuti ufulu wokana kulowa usilikali pa zifukwa za chipembedzo uyenera kulemekezedwa ngakhale pa nthawi yomwe pakufunika asilikali ambiri m’dziko. Kuchita zimenezi sikukutanthauza kuti munthu akungofuna kuzemba usilikali, kusalemekeza zimene boma likufuna kapena kusafuna kuti dziko likhale ndi chitetezo champhamvu. Zimene khoti lalikulu lachita pogwirizana ndi chigamulo cha khoti laling’ono zithandiza kwambiri kuti ufulu wa anthu a ku Ukrain utetezedwe. Dziko la Ukrain lapereka chitsanzo chabwino zedi ku mayiko amene amamanga anthu amene akana kulowa usilikali pa zifukwa za chipembedzo.