Anthu opalamula akamapanda kulangidwa, aliyense amaona kuti palibe vuto kupalamula. Izi n’zimene zikuchitika ku Ukraine, kumene a Mboni za Yehova ambiri akuchitiridwa zinthu zankhanza chifukwa chodana nawo. A Mboni za Yehova amayamikira kwambiri boma la Ukraine chifukwa linapereka ufulu wolambira kwa munthu aliyense. Komabe a Mboniwa akuda nkhawa chifukwa cha zinthu zankhanza zomwe akuchitiridwa ndi anthu ena ndiponso kuti boma silikumapereka chilango kwa anthu oterewa.

Zinthu Zankhanza Zikuchuluka

Kuyambira mu 2008, pachitika milandu 64 yokhudza a Mboni za Yehova ku Ukraine amene anavulazidwa pa nthawi imene ankachita kapena atangomaliza kumene kulambira kwawo. Pa milandu yonseyi, 16 inachitidwa ndi ansembe a tchalitchi cha Orthodox.

Kuyambira mu 2008 mpaka 2013 panali milandu 190 yokhudza kuwononga Nyumba za Ufumu ndipo anthu ankhanzawa anafuna kuwotcha nyumbazi maulendo 13. Chaka cha 2012 ndi 2013, milandu yokhudza kuwononga Nyumba za Ufumu inachuluka kuposa zaka 4 m’mbuyomo.

Kukula kwa milanduyi kukuwonjezekanso. Mu 2012, Nyumba za Ufumu ziwiri za m’chigawo cha Donetsk zinawonongedwa ndi moto, moti zinatheratu. Mu 2013, zinthu za nkhanza zimene zinachitika maulendo awiri zinapangitsa kuti a Mboni ena avulale kwambiri moti anakhala m’chipatala kwa nthawi yaitali.

A Mboni anadandaula kwa akuluakulu a boma pa zinthu zimene zikuwachitikirazi maulendo angapo. Komabe akuluakulu a bomawo safufuza mwachangu kapena mokwanira komanso sapereka chilango kwa anthu olakwawo.

Akuluakulu a Boma Akulekerera

Kuwotchedwa komanso kuwonongedwa kwa Nyumba ya Ufumu ku Horlivka m’dera la Donetsk pa June 5, 2014

Kuwonongedwa kwa katundu. Apolisi sakuchita chilichonse kapena akumabwera mochedwa akadziwitsidwa za zinthu zimene zachitika. Akuluakulu a boma akadziwitsidwa za mlandu winawake, iwo nthawi zambiri sakuchitapo chilichonse kapena akumazengereza kuti ayambe kufufuza. Ndipo mlandu ukayamba kuzengedwa, nthawi zambiri oweruza milandu akulephera kupereka chilango ndipo nthawi zinanso makhoti akumapereka chilango chofewa kwa olakwawo. Pa milandu 111 yokhudza kuwononga katundu yomwe yakhala ikuchitika kuyambira mu 2008 mpaka 2012, palibe mlandu womwe makhoti anaperekako chilango kwa anthu olakwa.

Kuvulazidwa. Nthawi zambiri apolisi safufuza bwinobwino milandu ndipo sayesetsa kuti agwire anthu omwe akuganiziridwa kuti ndi olakwa. Ndipo nthawi zambiri makhoti sapereka chigamulo chakuti olakwawo alipire ndalama zilizonse kapena kuti amangidwe. Makhoti akapereka chilango kwa anthu omwe ndi olakwa, nthawi zambiri chilango chake chimakhala chosagwirizana ndi kukula kwa milandu yomwe apalamula. Zimenezi zimachitika chifukwa chakuti akuluakulu a makhoti amanena kuti milanduyi sili m’gulu la milandu yokhudzana ndi chidani.

Zinthu zankhanza zikupitirirabe chifukwa chakuti anthu omwe akuchita zinthu zankhanzazo sakulangidwa

Kumenyedwa kwa a Oleksandr Tretiak

Bambo oleksandr Tretiak

Pa November 26, 2013, bambo Oleksandr Tretiak a zaka 41, omwe ndi a Mboni za Yehova, anamenyedwa kwambiri pamene ankabwerera kunyumba kwawo kuchokera kokalalikira. Anthu atatu anamenya bambowa mwankhanza kwambiri kwa maminitsi oposa 20. Bambo Oleksandr Tretiak, anazindikira kuti a Ruslan Ivanov, a Anatoliy Dovhan omwe kale anali mkulu wa apolisi ndi a Evheniy Ihlinskiy omwe amagwira ntchito monga wapolisi wa pamsewu komanso ndi mkamwini wawo wa a Anatoliy Dovhan ndi amene anawamenya. Ngakhale kuti anamenyedwa kwambiri, bambo Tretiak anakwanitsa kuthawa ndipo kenako anatengeredwa kuchipatala. Pa nthawiyi, thupi la bambowa linali ndi mabala aakulu ndiponso linali litanyuka kwabasi. Iwo anavulazidwanso muubongo komanso mphuno yawo inali itathyoka.

Ngakhale bambowa anavulazidwa chonchi, apolisi omwe ankafufuza nkhaniyi ananena kuti si mlandu waukulu chifukwa bambowa anavulazidwa pang’ono chabe ndi anthu atatu omwe sakudziwika bwinobwino. Patatha milungu iwiri, Bambo Tretiak anatulutsidwa m’chipatala ngakhale kuti anali asanachile. Akuluakulu a boma anaona kuti bambowa akakhalitsa m’chipatala zipereka umboni wakuti anavulazidwa kwambiri, choncho n’chifukwa chake iwo anatulutsidwa mofulumira pofuna kuti zimenezi zisadziwike. Popeza kuti Bambo Tretiak anamenyedwa kwambiri, zinachititsa kuti tsiku lotsatira agonekedwenso m’chipatala. Choncho masiku onse omwe bambowa anakhala m’chipatala anali 23.

Posachedwapa Bambo Ruslan Ivanov anayamba kuimbidwa mlandu wokhudza kumenyedwa kwa Bambo Tretiak koma anathawa mlanduwu. Bambo Tretiak akukhala mwamantha chifukwa akuopa kuti mwina anthuwa adzawachitanso chiwembu. Bambowa anati, “Sindikukayikira kuti anthu omwe anandivulazawo ankafuna kundipha ndipo anachita izi chifukwa chodana nane popeza ndine wa Mboni za Yehova.”

Kodi Akukuakulu a Boma Apitirizabe Kulekerera Zinthu Zoterezi?

Ku Ukraine kuli a Mboni za Yehova oposa 150,000, ndipo iwo akhala akutumikira Mulungu mosangalala chifukwa cha ufulu wolambira womwe uli m’dzikolo. Ndipo akuluakulu aboma akhala akuthandiza kwambiri a Mboni za Yehova m’mbuyomo pa nthawi yomwe ankazunzidwa. A Mboniwa akukhulupirira kuti akuluakulu a boma afufuza bwinobwino zinthu zankhanza zomwe zakhala zikuchitika ndipo apereka chilango chokwanira kwa anthu omwe akuchita zinthu zozunza a Mboni. Akukhulupiriranso kuti akuluakulu a boma aonetsetsa kuti anthu ochita zachiwawazi asapitirizenso kuchita zinthu zosalemekeza malamulo.