Pitani ku nkhani yake

Aibek Salayev, Matkarim Aminov, ndi Bahram Shamuradov anali gulu la a Mboni omwe anatulutsidwa m’ndende

NOVEMBER 13, 2014
TURKMENISTAN

Dziko la Turkmenistan Latulutsa M’ndende a Mboni Omwe Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Dziko la Turkmenistan Latulutsa M’ndende a Mboni Omwe Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Pa October 22, 2014, Pulezidenti Gurbanguly Berdimuhamedov analamula kuti anthu 8 a Mboni za Yehova omwe anamangidwa chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira atulutsidwe m’ndende. Pulezidentiyu analamulanso anthu ena omwe si a Mboni kuti atuluke m’ndende. Anthu 6 a Mboni anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira pomwe awiri anamangidwa pa milandu yongowanamizira yokhudzana ndi kuchita zinthu za chipembedzo chawo.

Merdan Amanov ndi Pavel Paymov

Anyamata amene anakana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupirirawa ndi a zaka za pakati pa 18 ndi 23 ndipo anatsekeredwa kundende yotchedwa Seydi Labor Colony, yomwe ili kuchipululu cha ku Turkmen. Merdan Amanov, Pavel Paymov, Suhrab Rahmanberdyyev, ndi Amirlan Tolkachev anaikidwa m’ndende imene anthu sakhala mozunzika kwambiri. Koma Matkarim Aminov ndi Dovran Matyakubov (zithunzi zawo sizinaonetsedwe) anaikidwa m’ndende imene anthu amakhala mozunzika kwambiri akuti chifukwa ndi akabwerebwere. Anyamatawa ankachitidwa zinthu zankhanza kwambiri komanso ankakhala moyo womvetsa chisoni nthawi imene anali kundende.

Amirlan Tolkachev

A Mboni awiri omwe anamangidwa pa milandu yongowanamizira aja ndi a Aibek Salayev, azaka 35 ndi a Bahram Shamuradov azaka 42. Nawonso anaikidwa kundende ya Seydi komwe anthu sakhala mozunzika kwambiri. Onse analamulidwa kuti akhale kundende zaka 4 chifukwa chochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo komanso zimene amakhulupirira. Pa nthawi imene anali kundende, anazunzidwa kwambiri ngakhale kuti anamangidwa pa mlandu wongowanamizira.

Panopa ndi wa Mboni mmodzi yekha, dzina lake Ruslan Narkuliev, amene adakali m’ndende ku Turkmenistan. Ruslan anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira patangotsala milungu yochepa kuti pulezidenti alamule zoti anthu ena atulutsidwe m’ndende. N’kutheka kuti dzina lake linali lisanatumizidwe kwa Pulezidenti nthawi imene ankalengeza za anthu oti atulutsidwe m’ndende. Anthu omuimirira pa mlanduwu akuyesetsa kukambirana ndi akuluakulu a ku Turkmen kuti nayenso amutulutse.

Pulezidenti Berdimuhamedov anachita zinthu zotamandika kwambiri polamula kuti anthu 8 omwe anamangidwa chifukwa chotsatira zimene amakhulupirirawa atuluke m’ndende. Anthu amene amalemekeza ufulu wachipembedzo akukhulupirira kuti uwu ndi umboni wakuti boma la Turkmenistan layamba kulemekeza ufulu wachipembedzo. Zimenezi zithandiza a Mboni za Yehova kuti azichita zinthu motsatira zimene amakhulupirira popanda kuopa kuti azunzidwa kapena kumangidwa.