Mayi Bibi Rahmanova, azaka 33 anaweruzidwa mopanda chilungamo kuti akakhale kundende pa milandu yongowanamizira. Chigamulochi chinaperekedwa ndi woweruza milandu wina dzina lake Gagysyz Orazmuradov, m’khoti la ku Dashoguz m’dziko la Turkmenistan. Pa August 18, mayi Bibi, omwe ali ndi mwana wazaka 4 akuti anapezeka olakwa chifukwa “chomenya wapolisi ndi kulalata.” * Oweruza anapereka chigamulo chokhwima choti kwa zaka 4, mayiwa akakhale kundende ya anthu opalamula milandu ikuluikulu.

Anagwidwa Ali ku Siteshoni ya Sitima

Nkhaniyi inachitika pa July 5, 2014 madzulo, pamene mayi Bibi ndi amuna awo a Vepa Tuvakov limodzi ndi mwana wawo wamwamuna anapita ku siteshoni yasitima ya ku Dashoguz kukatenga mabuku a chipembedzo chawo komanso zinthu zina zimene mnzawo wa ku Ashgabad anawatumizira. Banjali litangotenga chikwama momwe munali katundu wawoyo, apolisi 6 aamuna omwe sanavale yunifolomu, anawagwira ndipo anawauza kuti akufuna kuona zomwe zinali m’chikwamamo. Atayang’anamo, anapeza laputopu ndi mabuku a Mboni za Yehova. Nthawi yomweyo apolisiwo anayamba kuwakalipira ndi kuwaopseza kuti akachita masewera mwana wawo akhoza kukhala wamasiye.

Mayi Bibi anayamba kujambula zimene ankanenazo ndi foni ndipo anaibisa m’bulauzi pamene apolisiwo amafuna kuilanda. Zitatero apolisiwo anawakoka tsitsi, kuwamenya mateche kenako anawanyamula m’mwamba. Atawanyamula choncho, wapolisi wina anawavundukula bulauzi ndi kuwagwira mosayenera pamene ankalanda foni ija. Mayi Bibi anadzitchinjiriza kuti asawavulaze koma sanakane kumangidwa komanso sanamenye apolisiwo.

A Bibi, a Vepa ndi mwana wawo

Kenako apolisiwo anatengera banjali ku siteshoni ya apolisi. Atafika anakakamiza a Vepa kuti asaine sitetementi imene apolisiwo analemba koma anakana. Zitatero apolisiwo anayamba kumenya a Vepa mobwerezabwereza ndipo pa nthawiyi a Bibi ndi mwana wawo n’kuti ali m’chipinda china. Komabe a Vepa anakana kusaina ndipo apolisiwo anayambanso kukakamiza akazi awo kuti asaine. Atakana anawamenyanso kwambiri. Apolisiwo anatsekera a Bibi ndi mwana wawo n’kuwatulutsa tsiku lotsatira. * A Bibi atakadandaula kwa akuluakulu a ku Turkmen, a Vepa anatulutsidwa pa July 11, ndipo n’kuti patangodutsa masiku ochepa kuchokera tsiku limene anatsekeredwa. Kenako apolisi a mumzinda wa Dashoguz City, anayamba kufufuza za mlandu wa mayi Bibi ndi amuna awo.

Kupezedwa Olakwa, Kumangidwa Komanso Kuimbidwa Mlandu

Pa August 6 a Bibi anauzidwa kuti apezedwa olakwa, pa August 8 anatsekeredwa m’ndende ndipo anaimbidwa mlandu pa August 18. A Orazmuradov, omwe ankaweruza mlanduwu, anasonyezeratu kukondera pa nthawi imene mlanduwu unkazengedwa. Loya wa a Bibi akafuna kuti alankhule iwo ankangomudula mawu. Apolisi atapereka umboni wosiyana, woweruzayu sanalole kuti loya wa a Bibi awafunse mafunso. Anakanizanso a Vepa pomwe ankafuna kupereka umboni wa zinthu zachipongwe zimene apolisi anachitira a Bibi komanso anakana kumvetsera zinthu zimene anajambula zomwe zinachitika patsikulo. Kenako woweruzayo anapereka chigamulo chakuti a Bibi ndi olakwa ndipo akuyenera kukakhala kundende zaka 4.

Mayi Bibi anatsekeredwa ku malo osungira anthu oimbidwa mlandu a DZD-7 kudikira kuti achite apilo mlanduwu pa August 28. Apiloyi ikakanidwa, ndiye kuti asamutsidwira kundende ya anthu opalamula milandu ikuluikulu, ndipo mwina ikhoza kukhala ndende yomwe ili ku chipululu, ku Seydi. Zikatere aphwanyiridwa ufulu wawo wachibadwidwe komanso udindo wolera mwana wawo pa zaka zimene mwana amafunika kwambiri mayi ake.

Ngakhale kuti pakali pano a Vepa sanauzidwe kuti ndi olakwa, zikuoneka kuti akhoza kuuzidwanso kuti ndi olakwa, kuimbidwa mlandu wabodza komanso kuweruzidwa mopanda chilungamo kuti akakhale kundende. Ngati zimenezi zitachitika, ndiye kuti mwana wawo sakhala ndi mwayi woleredwa ndi mayi komanso bambo pa zaka zake zoyambirira. Kunena zoona, anthuwa akuzunzidwa popanda chifukwa.

Akufunitsitsa kuti Chilungamo Chioneke

Dziko la Turkmenistan limakonda kuchitira nkhanza a Mboni za Yehova komanso kuwaphwanyira ufulu wachibadwidwe. A Mboni za Yehova padziko lonse pamodzi ndi anthu ena ambiri amene amalemekeza ufulu wachibadwidwe wa anthu, monga ufulu wopembedza mwamtendere, akuyembekezera kuti boma la Turkmenistan lisiya kuphwanya ufulu wa anthu.

^ ndime 2 Munthu amene wapezeka ndi mlandu wolalatira kapena kukangana ndi munthu wosungitsa chitetezo amalamulidwa kuti akakhale ku ndende zaka 5.

^ ndime 6 Mwana wawo anakasiyidwa kwa achibale, m’mawa wa pa July 6 ndipo a Bibi anatulutsidwanso tsiku lomwelo chakumadzulo.