Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

SEPTEMBER 22, 2014
TURKMENISTAN

Mayi Wina Watulutsidwa Kundende M’dziko la Turkmenistan

Mayi Wina Watulutsidwa Kundende M’dziko la Turkmenistan

Bibi Rahmanova ndi banja lake

Pa September 2, 2014, mayi Bibi Rahmanova anatulutsidwa m’ndende 8 koloko madzulo. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti mlandu wawo watha. Pa tsikuli oweruza milandu a kukhoti la Dashoguz anagwiritsa ntchito apilo ya mayiyu koma sananene kuti milandu akuimbidwayo inali yabodza. Mmalo mwake anasintha chigamulo chimene anapatsidwa poyamba choti akakhale kundende kwa zaka zinayi kuti angokhala pa ukaidi wapakhomo wa zaka zinayi * ndipo analamula kuti atulutsidwe m’ndendemo nthawi yomweyo. Oweruzawa anachita zimenezi poganizira kuti mayi Bibi ndi munthu wamkazi, ali ndi mwana wamng’ono komanso alibe mbiri yoti anapalamulapo mlandu m’mbuyomu.

Mayi Bibi ananamiziridwa kuti “anamenya wapolisi” ndi “kumulalatira” ndipo pa August 18, khoti laling’ono linaweruza kuti ndi olakwa. Izi zinachititsa kuti apange apilo mlanduwu kukhoti lalikulu. Pa July 5, apolisi anagwira mwankhanza mayiwa ndi amuna awo a Vepa kusiteshoni yasitima ya ku Dashoguz. Banjali linali litangotenga katundu wawo kusiteshoniko yemwe anaphatikizapo mabuku a chipembedzo chawo. Patapita nthawi, apolisiwo ananena kuti a Vepa alibe mlandu koma akazi awo anakatsekeredwa kupolisi pa August 8. Pa nthawi imene anali m’ndendeyi, mayi Bibi anazunzidwa kwambiri.

Boma la Turkmenistan Laonetsa Poyera Kupanda Chilungamo Kwake

Zimene Loya wa mayi Bibi komanso mayiko ndi mabungwe ena ananena, zinathandiza kuti mayiwa atulutsidwe kundende.

Aka si koyamba kuti munthu wa Mboni achitidwe zinthu zopanda chilungamo ku Turkmenistan. A Mboni za Yehova ambiri amaphwanyiridwa ufulu wachibadwidwe m’dzikoli. Pakali pano a Mboni 8 ali m’ndende. Pa anthuwa, 6 anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira ndipo awiri pa zifukwa zongowanamizira. Anthuwa akukhala movutika kwambiri komanso akuzunzidwa m’njira zosiyanasiyana.

Ngakhale kuti oweruza mlandu a khoti la ku Dashoguz anayesetsa kuthandiza kuti mayi Bibi atuluke m’ndende, sanakwanitse kuthetsa zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitikira mayiyu. Anthu amene amalemekeza ufulu wachibadwidwe wa anthu akukhulupirira kuti boma la Turkmenistan lifufuza nkhaniyi mokwanira kuti chilungamo chioneke komanso kuti anthu azilambira mwaufulu m’dzikoli.

^ ndime 2 Khotili linasintha chigamulo choti mayi Bibi akakhale m’ndende kwa zaka 4, n’kulamula kuti angokhala pa ukaidi wapakhomo wa zaka zinayi. Koma zimenezi zikutanthauza kuti kwa zaka zitatu mayiwa akufunika kukhala ndi khalidwe labwino ndipo asasinthe dera lomwe akukhala kapenanso nyumba popanda chilolezo, n’cholinga choti akuluakulu a ndende aziyang’anira zochita zawo.