Pofika m’mwezi wa March, a Bahram Hemdemov adzakhala atakwanitsa chaka chimodzi kuchokera pamene anaikidwa m’ndende chifukwa chochita msonkhano wachipembedzo kunyumba kwawo mumzinda wa Turkmenabad, m’dziko la Turkmenistan. Pa 14 March 2015, apolisi anabwera kunyumba kwawo n’kuwagwira. Kenako anawamenya kwambiri n’kuwalamula kuti akhale m’ndende zaka 4 ndipo anawatumiza kundende ina ya m’tauni ya Seydi.

Malamulo a dziko la Turkmenistan amanena kuti munthu ali ndi ufulu “wopembedza payekha kapena pa gulu,” “wokhulupirira zimene akufuna ndiponso wouza ena zimene amakhulupirirazo.” Ngakhale zili choncho, a Bahram akukhalabe m’ndende ndipo akuzunzika kwambiri chifukwa chakuti ankachita zinthu zokhudza chikhulupiriro chawo. A Mboni za Yehova akupempha mwaulemu kuti boma litulutse a Bahram m’ndende.