Pitani ku nkhani yake

NOVEMBER 24, 2015
TURKMENISTAN

Dziko la Turkmenistan Linagamula Kuti a Bahram Hemdemov Akhale M’ndende Zaka 4 Chifukwa cha Chipembedzo

Dziko la Turkmenistan Linagamula Kuti a Bahram Hemdemov Akhale M’ndende Zaka 4 Chifukwa cha Chipembedzo

Pa 19 May 2015, khoti lina la ku Turkmenistan linagamula kuti a Bahram Hemdemov azaka 52, omwe ndi a Mboni za Yehova, akakhale kundende zaka 4 chifukwa chochita msonkhano wachipembedzo kunyumba kwawo mumzinda wa Turkmenabad. Pa nthawi imeneyi, apolisi anali atawasunga kale m’ndende kwa miyezi iwiri. Panopa, ali kundende ina ya m’tauni ya Seydi.

Apolisi Anaimitsa Msonkhano Wachipembedzo

Pa 14 March 2015, apolisi anaimitsa msonkhano wachipembedzo umene unachitikira kunyumba kwa a Hemdemov. Apolisiwa anachitira nkhanza anthu onse 38 amene anali pamsonkhanowo ndipo anawaimba mlandu wochita zinthu zachipembedzo zosemphana ndi malamulo. Iwo anamanga a Hemdemov n’kuwapanikiza ndi mafunso uku akuwamenya. Apolisi anawalanda katundu wawo monga galimoto, kompyuta ndi ndalama.

Kenako khoti lina la mumzinda wa Serdarabad linalipiritsa chindapusa a Mboni 30 n’kugamula kuti anthu 8 otsalawo akakhale m’ndende masiku 15. Mwana wa a Hemdemov dzina lake Serdar anagamulidwa kuti akakhale m’ndende masiku 30 ndipo anaikidwa m’chipinda chayekha. Anamupanikizanso ndi mafunso, kumumenya kwambiri ndiponso kumuzunza. Khotili linagamulanso kuti wa Mboni wina dzina lake Emirdzhan Dzhumnazarov akhale m’ndende masiku 30 ndipo ankamenyedwa komanso kuopsezedwa.

Pa 19 May 2015, woweruza anaimba a Bahram Hemdemov mlandu wabodza wakuti “ankalimbikitsa anthu kudana ndi anthu ena azipembedzo zina” ndipo linagamula kuti akakhale m’ndende zaka 4. Pa 10 June 2015, a Hemdemov anawasamutsa m’ndende ya ku Turkmenabad n’kuwapititsa kundende ya ku Seydi.

Woyang’anira ndendeyo sankalola aliyense, kuphatikizapo achibale, kuti adzaone a Hemdemov, mpaka nthawi yoti angachite apilo itadutsa. Anachita zimenezi n’cholinga choti a Hemdemov kapena wina aliyense asachite apilo mlanduwo. Kuchokera nthawi imene a Hemdemov anamangidwa, apolisi akhala akuwapatsa ntchito yakalavulagaga ndiponso kuwakakamiza kuti avomere zoti anachitadi zinthu zosemphana ndi malamulo. Akhalanso akuwamenya kwambiri pofuna kuwabwezera chifukwa chakuti mkazi wawo analemba chikalata chopita kukhoti chodandaula za nkhanza zimene a Hemdemov ankachitiridwa.

Mkazi wa a Hemdemov anachita apilo mlanduwu kukhoti lalikulu la m’dzikolo. Ngakhale kuti panalibe umboni uliwonse woti analakwira boma, wachiwiri kwa tcheyamani wa khotili ananena kuti sangalole apiloyo chifukwa panalibe zifukwa zomveka. Chakumayambiriro kwa mwezi wa August, loya wa a Hemdemov anachitanso apilo. Koma pa 25 August 2015, khoti lalikulu linakananso apiloyo ponena kuti a Hemdemov “amalimbikitsa zikhulupiriro za Mboni za Yehova.”

“Akuluakulu a boma la Turkmenistan achita zinthu zambiri zopanda chilungamo. . . . Khoti lalikulu la ku Turkmenistan linalephera kuthandiza a Bahram Hemdemov pa zinthu zopanda chilungamo zimene zinawachitikira.”—A Philip Brumley, omwe ndi loya wa Mboni za Yehova.

Apolisi Ankachitira Nkhanza Anthu ku Turkmenabad

Pofika chakumapeto kwa chaka cha 2014, akuluakulu a boma la Turkmenistan anali atayamba kupatsa a Mboni za Yehova ufulu wopembedza. Mu September 2014 a Bibi Rahmanova, omwe anaikidwa m’ndende pa mlandu wabodza, anatulutsidwa ndipo n’kuti atakhala m’ndende kuyambira mu August 2014. Mu October 2014, boma linamasulanso a Mboni ena 8 omwe anali atamangidwa chifukwa chochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo. Ngakhale kuti akuluakulu ena aboma akupereka ufulu kwa a Mboni, pali ena amene akumangabe ndiponso kuchitira nkhanza a Mboni ku Turkmenabad.

Pa 6 February 2015, apolisi anamanga a Mboni 4 omwe mayina awo ndi Viktor Yarygin, Rustam Nazarov, Charygeldy Dzhumaev ndi Jamilya Adylova. Onsewa anaimbidwa mlandu wakuti “akuvutitsa anthu” chifukwa choti anapezeka ndi mabuku achipembedzo chawo. Akuluakulu a Unduna wa Zachitetezo anamenya atatu mwa a Mboniwa, kuphatikizapo mayi Adylova. Anamenya a Dzhumaev kwambiri moti anakomoka kangapo. Khoti la mumzinda wa Turkmenabad linalipiritsa chindapusa a Yarygin n’kulamula kuti a Nazarov akhale m’ndende masiku 30 komanso kuti a Dzhumaev ndi mayi Adylova akhale m’ndende masiku 45. * A Mboniwa atumiza chikalata chodandaula za zimenezi ku ofesi ya pulezidenti ndiponso ofesi ya loya wa boma ku Ashgabad.

Patapita milungu iwiri, apolisi anapita kunyumba ya a Zeynep Husaynova kuti akafufuze ngati ali ndi mabuku omwe amati ndi “osavomerezeka.” Apolisiwa analanda mabuku awo komanso kuwaopseza kuti awagwira ndipo akakhala m’ndende masiku 15.

Wa Mboni wina dzina lake Dovlet Kandymov anaimbidwa mlandu wochita zinthu zosavomerezeka zokhudza chipembedzo ndipo anakhala m’ndende masiku 45. Ali m’ndende, apolisi ankamumenya kawirikawiri chifukwa choti ankakana kupereka umboni umene ukanachititsa kuti a Bahram Hemdemov aoneke ngati olakwa.

Kodi Dziko la Turkmenistan Litsatira Zimene Linalonjeza Zolemekeza Ufulu Wachipembedzo?

Patapita kanthawi, akuluakulu a boma ku Turkmenabad anasiya kuzunza a Mboni za Yehova. Koma a Bahram Hemdemov, sanawatulutsebe m’ndende mpaka pano, akuti chifukwa choti ankachita zachipembedzo.

A Bahram Hemdemov ali ndi mkazi wawo ndiponso mwana wawo wina

Malamulo a dziko la Turkmenistan amanena kuti munthu ali ndi ufulu “wopembedza payekha kapena pa gulu” komanso “wokhulupirira zimene akufuna n’kuuza ena zimene amakhulupirirazo.” Choncho boma la m’dzikoli liyenera kulola anthu, kuphatikizapo a Mboni za Yehova, kuti azichita zachipembedzo chawo mwaufulu. Dziko la Turkmenistan linavomerezanso Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale lomwe limanena kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wotha kukhala ndi maganizo osiyana ndi anthu ena, wotsatira zimene amakhulupirira ndiponso wopembedza.

A Philip Brumley omwe ndi loya wa Mboni za Yehova anati:

Akuluakulu a boma la Turkmenistan achita zinthu zambiri zopanda chilungamo. Apolisi a ku Turkmenabad anaphwanya malamulo posokoneza msonkhano wachipembedzo n’kuchitira nkhanza anthu omwe anali pamsonkhanowo. Akuluakulu a khoti la ku Turkmenabad anavomereza zimene apolisiwo anachita. Komanso khoti lalikulu la ku Turkmenistan linalephera kuthandiza a Bahram Hemdemov pa zinthu zopanda chilungamo zimene zinawachitikira.

A Mboni za Yehova akupempha kuti boma la ku Turkmenistan liwalole kuti alembetse chipembedzo chawo m’kaundula, lilole kuti a Mboniwo azipembedza mwaufulu ndiponso kuti asamachitiridwe nkhanza ngati mmene zinachitikira ku Turkmenabad chakumayambiriro kwa chaka chino. Akupemphanso boma kuti limasule a Bahram Hemdemov kuti abwerere kwawo.

A Mboni za Yehova akuthokoza boma la Turkmenistan chifukwa cha zimene lakhala likuchita m’mbuyomu pomasula anthu osalakwa amene anamangidwa. Koma boma lingachite bwino kumasulanso a Bahram Hemdemov posonyeza kuti likuonetsetsa kuti anthu onse ali ndi ufulu wopembedza.

^ ndime 11 Malamulo a ku Turkmenistan amanena kuti munthu akapezeka kuti ndi wolakwa pa mlandu wakuti “akuvutitsa anthu” ayenera kupatsidwa chilango chokhala m’ndende masiku osapitirira 15. Koma khoti linagamula kuti a Dzhumaev ndi mayi Adylova akhale m’ndende masiku 45.