Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MAY 3, 2016
TURKMENISTAN

Apolisi ku Turkmenabad Anachitira Nkhanza a Mboni Omwe Ankachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu

Apolisi ku Turkmenabad Anachitira Nkhanza a Mboni Omwe Ankachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu

Pa 23 March, 2016, a Mboni za Yehova okwana 20 ku Turkmenabad m’dziko la Turkmenistan anasonkhana m’nyumba ina kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu womwe amachita chaka chilichonse . Mwambowu uli mkati, panafika gulu la apolisi limene linkafuna kudzasokoneza koma analephera kulowa m’kati. Atalephera kulowa, apolisiwo anangokhala kunja osachoka. Palibe wa Mboni amene anayerekeza kutuluka moti onse anakhalabe mkati momwemo mpaka m’mawa.

Kutacha, apolisi 4 anathyola chitseko n’kulowa m’nyumbamo n’kuyamba kuzunza ena mwa a Mboniwo mpaka anavulaza mayi wina woyembekezera moti anafunika kupita naye ku chipatala. Apolisiwo anatenga a Mboniwo n’kukawatsekera ndipo kumeneko anamenya abambo awiri omwe anali m’gululo. Pa 25 March, apolisiwo anatulutsa a Mboniwa kupatulapo bambo m’modzi amene anamusungabe m’ndendemo kwa masiku 15. Pa 19 April, akuluakulu a boma analipiritsa a Mboni 7 omwe anali m’gululi, aliyense ndalama zokwana madola 143 a ku America ngakhale kuti sanawazenge mlandu ku khothi.