Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

ZOKHUDZA MALAMULO NDIPONSO UFULU WACHIBADWIDWE

Zokhudzana ndi Malamulo ku Turkey

JUNE 3, 2016

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula kuti Dziko la Turkey Liyenera Kuvomereza Nyumba za Ufumu Monga “Malo Olambirira”

Ngakhale kuti zinthu zakhala zikuyenda bwino kwa a Mboni za Yehova pankhani zamalamulo, iwo akuvutikabe chifukwa malamulo a dziko la Turkey sakuwalola kumanga komanso kukhala ndi malo olambirira ovomerezeka.

JUNE 11, 2014

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula Mlandu Wina Mokomera Anthu 4 a Mboni ku Turkey

Zimene khoti lachita poweruza mlandu wachitatu mosakomera boma la Turkey zikusonyezeratu kuti mayiko onse amene ali m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya, akuyenera kutsatira mfundo zimene zili m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya, zomwe zimasonyeza kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali.

MARCH 17, 2014

Dziko la Turkey Likukana Kutsatira Mfundo Zimene Mayiko a ku Ulaya Amayendera Zokhudza Ufulu wa Anthu

N’chifukwa chiyani boma likukana kulemekeza ufulu umene anthu ali nawo wokana kulowa usilikali, womwe ndi ufulu wofunika kwambiri wokhudza ufulu wachibadwidwe?