Pa 13 April, 2018, a Daniil Islamov omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, anamasulidwa m’ndende ya Yavan pambuyo pogwira ukaidi kwa miyezi 6. Bambo Islamov anakhala m’ndende pafupifupi chaka chimodzi chifukwa poyamba ankangosungidwa kaye m’ndendemo kwa miyezi 6 poyembekezera kuwazenga mlandu.

Mu April 2017, a Islamov anaitanidwa kuti akayambe ntchito yausilikali ndipo anapitadi ku ofesi yomwe anthu amalembetsera usilikali. Koma iwo anauza asilikaliwo kuti sangagwire ntchito ya usilikali chifukwa ntchitoyi ndi yosemphana ndi chikumbumtima chawo. Kenako asilikali ena anamanga bambo Islamov ndi kuwasunga ku kampu ya asilikali mpaka pa nthawi yozenga mlandu wawo. Pa nthawi yonse yomwe anasungidwayi, ankawakakamiza kuti alumbire kuti alowa usilikali komanso kuti azivala yunifolomu ya usilikali, koma anakana kuchita zonsezi.

M’dziko la Tajikistan, muli lamulo limene limalola munthu kugwira ntchito zina ngati sakufuna kulowa usilikali koma boma silinavomereze kuti lamuloli lizigwira ntchito. Ndiye poti bambo Islamov amangosungidwa kundende chifukwa chokana kulowa usilikali, iwo analemba kalata yodandaula n’kuipereka ku Gulu la Bungwe la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka. (UN Working Group on Arbitrary Detention) Pa 5 October, 2017, gululi linanena maganizo ake pa nkhaniyi ndipo linati kukana usilikali chifukwa cha chikumbumtima ndi ufulu wa munthu umene mayiko ambiri amautsatira. Ndipo linamaliza n’kunena kuti boma la Tajikistan lili ndi mlandu posunga bambo Islamov m’ndende ndipo liyenera kuwamasula mwamsanga.

Komabe, dziko la Tajikistan silinatsatire zimene gululi linagamula. Ndipo pa 13 October, 2017, khoti la asilikali la ku Tajikistan linalamula bambo Islamov kuti akhale m’ndende kwa miyezi 6. Bungwe la asilikali a Khoti Lalikulu Kwambiri linakana apilo yomwe bambo Islamov anapanga ndipo anagwira ukaidi miyezi yonse 6.

A Philip Brumley omwe ndi Loya Woimira Mboni za Yehova anati: “Tikukhulupirira kuti boma la Tajikistan liunikanso zomwe limachitira anthu omwe akana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira monga mmene lachitira ndi bambo Islamov. Popeza kuti Gulu la Bungwe la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka komanso makhoti a mayiko ena analamula mobwerezabwereza kuti kukana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima ndi ufulu womwe mayiko ambiri amautsatira, tikuyembekezera kuti dziko la Tajikistan litsatira zomwe linalonjeza kuti lizilemekeza ufulu wa anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo.”