Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MAY 18, 2015
SOUTH KOREA

Woweruza Milandu ku South Korea Anagamula Kuti Anthu Amene Anakana Usilikali Alibe Mlandu

Woweruza Milandu ku South Korea Anagamula Kuti Anthu Amene Anakana Usilikali Alibe Mlandu

Pa 12 May 2015, khothi la ku Gwangju linagamula kuti a Mboni za Yehova ena atatu ndi osalakwa pa mlandu wokana kulowa usilikali. Woweruza milandu wamkulu pa khotili dzina lake Choi, Chang-seok anafotokoza chigamulo chake kuti: “Tingamvetse bwino ufulu umene munthu ali nawo wotsatira zimene amakhulupirira tikaona zimene malamulo amanena komanso zimene zimafunika pa nkhani ya chitetezo cha dziko.” Iye ananenanso kuti: “Ngati malamulo amafuna kuti munthu achite zinazake ndipo pa nthawi yofananayo munthuyo ali ndi ufulu wokana kapena kuvomera kuchita zimenezo ndiye kuti malamulowo ayenera kutsatiridwa mokomera mbali zonse.” A Mboni akuyembekezera kuti woimira boma pa mlanduwu achita apilo pasanathe masiku 7.