Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

SOUTH KOREA

Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

A Mboni za Yehova akhala akusangalala ndi ufulu wa kulambira m’dziko la South Korea kwa zaka zoposa 100. Koma anyamata a Mboni sasangalala ndi ufuluwu chifukwa amaumirizidwa kuti alowe usilikali zomwe ndi zosemphana ndi zimene amakhulupirira. Akakana amamangidwa moti chaka chilichonse anyamata ambiri a Mboni za Yehova amamangidwa. Kwa zaka zonsezi, boma la South Korea silinakhazikitse ntchito zoti anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azigwira. Zimenezi zapangitsa kuti anyamata a Mboni oposa 18,000 amangidwe ndipo tikaphatikiza zaka zimene onse pamodzi akhala m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali zikuposa 34,700.

Zinthu Zayamba Kusintha M’ndende

Kale a Mboni akamangidwa ankakhala mozunzika kwambiri kundende komanso amakhalako nthawi yaitali. Koma panopa sakukhalako mozunzika kwambiri komanso nthawi yokhalako yafupikitsidwa moti akumakhalako miyezi 18. Akuluakulu a kundende akumalola a Mboni ambiri kuti azipanga misonkhano yawo kundende. Kuwonjezera pamenepa, akaidi ambiri a Mboni analekanitsidwa ndi akaidi ena ndipo anaikidwa m’zipinda limodzi ndi a Mboni anzawo. *

Zimene Mayiko Ambiri Amanena Zokhudza Ufulu Wokana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Munthu Amakhulupirira

Komiti ya bungwe la United Nations yoona za ufulu wachibadwidwe (Human Rights Committee [CCPR]), imene imaonetsetsa kuti mayiko akutsatira mfundo za mu Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale (ICCPR), yakhala ikunena mobwerezabwereza kuti dziko la South Korea * likuphwanya ufulu wa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Mwachitsanzo, pa October 25, 2012, Komitiyi inapeza kuti malinga ndi Gawo 18, dziko la South Korea linaphwanya ufulu wa a Mboni za Yehova 388 omwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Komitiyi inanena kuti “ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira ndi wofanana ndi ufulu wonena maganizo ako, ufulu wotsatira zimene umakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza. Ufuluwu umapatsa munthu mwayi wokana kulowa usilikali ngati munthuyo akuona kuti n’zosagwirizana ndi chipembedzo chake kapena zimene amakhulupirira.” Boma la South Korea likupitiriza kuphwanya ufulu wonena maganizo ako, ufulu wotsatira zimene umakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza wa anyamata ambiri a Mboni amene bomali likuwamanga. Choncho n’zoonekeratu kuti sakutsatira mfundo za komitiyi.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. October 31, 2014

  A Mboni za Yehova 597 ali m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupira.

 2. August 31, 2014

  A Mboni za Yehova 562 ali m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupira.

 3. June 30, 2014

  Milandu 28 yokhudza anthu amene anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira inatumizidwa kukhoti lalikulu la m’dzikoli ndipo anyamata a Mboni 618 anamangidwa.

 4. January 28, 2014

  Pulezidenti wa Dziko la South Korea anakhazikitsa lamulo loti anyamata a Mboni oposa 100 achotseredwe mwezi umodzi kapena iwiri pa nthawi imene anayenera kukhala m’ndende. Anyamatawa anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira; pa 31 January anyamata 513 anamangidwa.

 5. November 2013

  A Mboni 599 anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

 6. April 2013

  A Mboni za Yehova 70 pa 100 alionse analekanitsidwa ndi akaidi ena ndipo anaikidwa m’zipinda limodzi ndi a Mboni anzawo.

 7. October 25, 2012

  Komiti ya bungwe la United Nations yoona za ufulu wachibadwidwe (Human Rights Committee [CCPR]), inapeza kuti malinga ndi Gawo 18, dziko la South Korea linaphwanya ufulu (wonena maganizo ako, ufulu wotsatira zimene umakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza) wa a Mboni za Yehova 388 omwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

 8. August 30, 2011

  Khoti lalikulu la ku South Korea linanena kuti malamulo omanga anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira si osemphana ndi malamulo a dziko la Korea.

 9. March 24, 2011

  Komiti ya bungwe la United Nations yoona za ufulu wachibadwidwe (Human Rights Committee [CCPR]) inapeza kuti malinga ndi Gawo 18, dziko la South Korea linaphwanya ufulu wa a Mboni za Yehova 100 wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

 10. January 15, 2009

  Komiti imene pulezidenti wa dzikoli anakhazikitsa kuti ifufuze za anthu osalakwa amene anaphedwa, inatulutsa lipoti lotsimikizira kuti boma la South Korea linkakhudzidwa ndi imfa ya anyamata a Mboni 5 amene anaphedwa m’zaka za pakati pa 1975 ndi 1985. Anyamatawa anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

 11. December 2008

  Dziko la South Korea linasintha mapulani ofuna kukhazikitsa ntchito zoti anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azigwira.

 12. September 18, 2007

  Unduna wa Zachitetezo wa dziko la South Korea unalengeza kuti ukupanga mapulani okhazikitsa ntchito zoti anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azigwira ndipo analonjeza kuti asintha malamulo okhudza kuphunzira komanso kulowa usilikali.

 13. November 3, 2006

  Komiti ya bungwe la United Nations yoona za ufulu wachibadwidwe (Human Rights Committee [CCPR]) inapeza kuti malinga ndi Gawo 18, la Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale (ICCPR) dziko la South Korea linaphwanya ufulu wa a Mboni za Yehova awiri, wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

 14. August 26, 2004

  Khoti lalikulu la dziko la South Korea linanena kuti lamulo lomanga anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndi logwirizana ndi malamulo a dzikoli.

 15. 2001

  Ofesi yoona zolemba anthu ntchito ya usilikali inasiya kulemba anthu usilikali mokakamiza ndipo nthawi yokhala kundende inachepetsedwa kuchokera pa zaka zitatu kufika pa chaka ndi hafu.

 16. December 1, 1985

  Kim, Young-geun anamwalira chifukwa chochitidwa zinthu zankhanza kwambiri ndi asilikali nthawi imene anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

 17. August 17, 1981

  Kim, Sun-tae anamwalira chifukwa chochitidwa zinthu zankhanza kwambiri ndi asilikali nthawi imene anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

 18. March 28, 1976

  Jeong, Sang-bok anamwalira atamenyedwa mwankhanza komanso kuzunzidwa ndi asilikali chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

 19. March 19, 1976

  Lee, Choon-gil anamwalira atamenyedwa mwankhanza ndi apolisi, chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira, mpaka anang’ambika kapamba.

 20. November 14, 1975

  Kim, Jong-sik anamwalira atamenyedwa kwambiri ndi msilikali chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

 21. 1975

  Pulezidenti Park Jeong-Hee anakhazikitsa lamulo loti munthu wamwamuna aliyense azilowa usilikali ndipo palibe ankaloledwa kukana. Anyamata a Mboni ankapititsidwa mokakamiza ku malo ochitira za usilikali.

 22. January 30, 1973

  Anakhwimitsa chilango chimene anthu okana kulowa usilikali azilandira, moti anaonjezera nthawi imene anthu okana kulowa usilikali azikhala m’ndende kuchoka pa zaka zitatu kufika pa zaka 10. Anthu ena ankakakamizidwa kulowa usilikali maulendo angapo.

 23. 1953

  Dziko la South Korea linayamba kumanga anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

^ ndime 6 Dziko la South Korea lili mu Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale (ICCPR) komanso linavomereza kulola nzika za dzikoli kutumiza dandaulo lawo ku Komiti ya bungwe la United Nations yoona za ufulu wachibadwidwe (Human Rights Committee [CCPR]) ngati dzikoli laphwanya ufulu wawo.