Pitani ku nkhani yake

MARCH 1, 2018
SOUTH KOREA

Makhoti a ku South Korea Akufufuza Njira Yabwino Yochitira Zinthu ndi Anthu Okana Usilikali

Makhoti a ku South Korea Akufufuza Njira Yabwino Yochitira Zinthu ndi Anthu Okana Usilikali

M’malo mongomanga a Mboni za Yehova amene amakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, oweruza ku South Korea akufufuza njira imene angawathandizire. Oweruza ena amaganizira cholinga cha a Mboniwa chomwe ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi Malemba komanso kupewa kuchita zinthu zopweteka anthu ena. * Choncho makhoti ena amatsatira mfundo yoti anthu onse ali ndi ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira ndipo anagamula kuti a Mboniwa alibe mlandu wokana usilikali popanda chifukwa chomveka. M’mbuyomo chigamulo choti a Mboni ndi osalakwa chinangoperekedwa maulendo 4 okha, koma kuyambira mu May 2015, oweruza ena anagamula maulendo 66 kuti a Mboni ndi osalakwa.

Chigamulo Chimene Chingasinthe Zinthu

Pa 1 February 2018, khoti la apilo ku Busan linasankha kuyendera chigamulo cha khoti lina chomwe chinali choti wa Mboni anali wosalakwa. Pochita zimenezi, khotili linanyalanyaza mfundo za khoti lalikulu komanso khoti loona za malamulo m’dzikoli. Chigamulo cha khoti la ku Busan chinali chodabwitsa pa zifukwa ziwiri. Choyamba, khoti limeneli limadziwika kuti ndi lokhwimitsa zinthu. Chachiwiri, woweruza wake wamkulu, dzina lake Jong-du Choi, anali atagamulapo m’mbuyomu kuti munthu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndi wolakwa.

Oweruza atatu amene anagamula pa nkhaniyi anaganizira kwambiri udindo wa dziko la South Korea wotsatira malamulo apadziko lonse omwe dzikoli linavomereza. Mwachitsanzo, dzikoli linavomereza Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale, lomwe limapatsa anthu ufulu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Khotili linaona kuti “kumanga anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira kumatsutsana ndi chigawo 18 cha panganoli, choncho . . . kukana usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira ndi “chifukwa chomveka.” Chigamulo cha khotili chinadziwika kwambiri ndipo anthu ambiri akukhulupirira kuti chithandiza kusintha mmene makhoti ena amaweruzira pa nkhaniyi.

Akuyembekezera Zimene Khoti Loona za Malamulo Lingagamule

Chaka chilichonse, oweruza ankagamula kuti anyamata okwana 500 kapena 600, omwe akana usilikali chifukwa za zimene amakhulupirira, apite kundende. Koma panopa oweruza ambiri akuzengereza kugamula pa nkhaniyi. Pali milandu yoposa 700 imene sinagamulidwebe chifukwa chakuti oweruza akudikira chigamulo chochokera kukhoti loona za malamulo. Pa 31 December 2017, kunali anyamata a Mboni okwana 267 okha amene anali mundende, ndipo chiwerengero chimenechi ndi chotsika kwambiri pa zaka 10 zapitazi.

Khoti loona za malamulo liyenera kuganizira zinthu ziwiri pogamula pa nkhaniyi. Choyamba, liyenera kuganizira ngati oweruza ayenera kuona anthu amene amakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira kuti ndi oyenera kulangidwa mogwirizana ndi malamulo okhudza kukana usilikali. Chachiwiri, liyenera kuganizira ngati anthuwo akutetezedwa ndi malamulo apadziko lonse omwe amapatsa anthu ufulu wotsatira zimene amakhulupirira. Anthu ambiri ku South Korea akuyembekezera kuti khotili lipeza njira yothetsera vutoli yomwe ilemekeze anyamata amene amakana usilikali koma akhoza kugwira ntchito ina yothandiza dzikoli yomwe ndi yosakhudza usilikali.

Ngati khotili lingagamule nkhaniyi mokomera anthu okana usilikali ndiye kuti dziko la South Korea likhala logwirizana ndi zimene Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu yachita ndi milandu yambiri pa nkhaniyi. Komitiyi yapempha dziko la South Korea kuti lisiye kumanga anthu okana usilikali koma liyambe kulemekeza ufulu wawo wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.

^ ndime 2 Mwachitsanzo, lemba la Yesaya 2:4 limanena kuti: “Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.” Nayenso Yesu analamula otsatira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:34, 35.