Pitani ku nkhani yake

FEBRUARY 9, 2016
SOUTH KOREA

Komiti ina ya United Nations Yapempha Dziko la South Korea Kuti Lipereke kwa Anthu Ufulu Wokana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Komiti ina ya United Nations Yapempha Dziko la South Korea Kuti Lipereke kwa Anthu Ufulu Wokana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu itafufuza zimene dziko la South Korea likuchita pa nkhani ya ufulu wa anthu, inapereka chigamulo chake pa 3 November 2015. Komitiyi inavomera kuti pali zinthu zina zimene boma la South Korea likuchita bwino pa nkhani yopereka ufulu kwa anthu. Koma inapeza kuti bomali likulephera kutsatira zimene komitiyi inali itagamula kale zokhudza anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Ufulu Wachipembedzo Komanso Wochita Zimene Umakhulupirira

Ngakhale kuti mayiko apadziko lonse amaona kuti anthu ayenera kupatsidwa ufulu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, dziko la South Korea likupitiriza kupereka chilango kwa anthu okana usilikali. Kuchokera mu 1950, makhoti a m’dzikoli anagamula kuti a Mboni za Yehova oposa 18,000 akakhale kundende. Tikaphatikiza pamodzi zaka zimene anthu onsewa anagamulidwa kuti akhale m’ndende zimakwana 36,000.

Lipoti la Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu linapempha boma la South Korea kuti:

  • Litulutse mwamsanga anthu onse amene anawamanga chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

  • Lifufute mayina a anthuwo m’kaundula wa anthu opalamula milandu, liwapatse chipukuta misozi komanso lisafalitse zinthu zachinsinsi zokhudza anthuwo.

  • Likonze malamulo ake kuti aziteteza anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira komanso liziwapatsa mwayi woti azigwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali.

Dziko la South Korea Liyenera Kutsatira Pangano Limene Linasainira

Kuchokera mu 2006, Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapereka zigamulo 5 zodzudzula boma la South Korea. Inachita zimenezi chifukwa choti bomali linalephera kukhazikitsa malamulo oteteza ufulu wa anthu wokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira komanso chifukwa choti linapereka chilango kwa anthuwo. * Lipoti laposachedwapa la komiti ya United Nations linapemphanso bomali kuti “likhazikitse njira zabwino zothandiza kuti lizitsatira zigamulo zimene komitiyi yapereka,” kuphatikizapo zomwe inapereka kale.

Lipotili litatulutsidwa, a Seong-ho Lee, omwe ndi tcheyamani wa Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea, anavomereza zimene zinalembedwa m’lipotilo zoti ufulu wa anthu unkaphwanyidwa. A Lee analangiza boma la South Korea kuti litsatire zigamulo za komitiyi ndipo anati: “Boma lili ndi udindo wotsatira zonse zimene zili m’Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale.”

Popeza kuti boma la South Korea linasainira Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale, lili ndi udindo woteteza ufulu womwe uli m’panganoli. Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu imaonetsetsa kuti mayiko azitsatira panganoli komanso imateteza ufulu wa anthu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Choncho komitiyi ipitiriza kudzudzula dziko la South Korea chifukwa chonyalanyaza panganoli ngati silitsatira zigamulo zimene komitiyi yapereka.

Lipoti limene Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu latulutsa ndi limodzi mwa zimene mayiko enanso akhala akudandaula zokhudza nkhanza zimene dziko la South Korea likuchitira anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Chifukwa cha zimenezi, anthu a m’dzikoli komanso a m’mayiko ena ali ndi chidwi choti aone ngati boma la South Korea lichitepo kanthu pa zimene zili m’lipotili.

^ ndime 10 Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu imapereka zigamulo zake ikafufuza ngati dziko lina lomwe linasainira Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale likutsatira panganoli kapena ayi. Zigamulo 5 zimene komitiyi inapereka zosonyeza kuti dziko la South Korea linaphwanya Gawo 18 lokhudza, “ufulu wonena maganizo ako, wotsatira zimene umakhulupirira komanso wachipembedzo” ndi Mlandu Na. 1321-1322/2004 wa Pakati pa Yeo-bum Yoon Ndiponso Myung-jin Choi ndi Dziko la South Korea, wogamulidwa pa 3 November 2006; Mlandu Na. 1593-1603/2007, wa Pakati pa Eu-min Jung et al. ndi Dziko la South Korea, wogamulidwa pa 23 March 2010; Mlandu Na. 1642-1741/2007, wa Pakati pa Min-kyu Jeong et al. ndi Dziko la South Korea, wogamulidwa pa 24 March 2011; Mlandu Na. 1786/2008, wa Pakati pa Jong-nam Kim et al. ndi Dziko la South Korea, wogamulidwa pa 25 October 2012 komanso Mlandu Na. 2179/2012, wa Pakati pa Young-kwan Kim et al. ndi  Dziko la South Korea, wogamulidwa pa 15 October 2014.