Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

12 OCTOBER, 2016
SOUTH KOREA

Akuvutika Chifukwa Chakuti Anakana Usilikali Potsatira Zomwe Amakhulupirira

Akuvutika Chifukwa Chakuti Anakana Usilikali Potsatira Zomwe Amakhulupirira

Mu January 2016, anyamata awiri, Hyun-jun Gwon ndi Gwang-taek Oh, anakwera ndege yochokera ku South Korea kupita ku Japan kuti akasangalaleko kutchuthi. Atafika pabwalo la ndege la Nagoya ku Japan, anapita pamaofesi oona za anthu otuluka komanso kulowa m’dziko ndipo ankaganiza kuti zonse ziyenda bwino. Koma akuluakulu a pamalowa anayamba kuwapanikiza ndi mafunso ataona kuti makadi awo akusonyeza kuti nthawi ina anazengedwapo mlandu.

Achinyamatawo anavomera kuti anaponyedwapo m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zomwe amakhulupirira ndipo mlandu wawowo unatha. Ananenanso kuti mayiko ambiri amavomereza kuti munthu azikhala ndi ufulu pa nkhani imeneyi. Koma akuluakuluwo anakana kuwalola kuti alowe m’dziko la Japan. Achinyamatawo anayesa kukambirana ndi kazembe wa dziko la Japan ku South Korea koma sizinathandize ndipo anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa chosonyeza kulimba mtima poikira kumbuyo chikhulupiriro chawo.

Mavuto Omwe Anthu Okana Usilikali Amakumana Nawo

Dziko la South Korea linaika lamulo loti munthu amene akukana usilikali azisankha chimodzi: Kulolera kuyamba usilikali kapena kupita kundende. Boma la South Korea likuphwanya mfundo zimene mayiko ambiri amayendera pa nkhani zokhudza ufulu wa anthu ndipo silipereka mwayi wogwira ntchito zina kwa anthu okana usilikali. * Ku South Korea, munthu akakana usilikali, mlandu wake sutha ndipo bomali limakana kuthetsa lamulo lomwe linaika pa nkhaniyi ngakhale kuti kuchita zimenezi n’kuphwanya ufulu wa anthuwo. Munthu woteroyo amavutikabe ngakhale kuti anagwira kale ukaidi. Mbiri yoti munthuyo anakhalako m’ndende chifukwa chokana usilikali, imachititsa kuti asakhale ndi mwayi wolembedwa ntchito zina komanso amalephera kupita kumayiko ena ngati ku Japan kumene anthu ambiri a ku South Korea amakonda kupita.

Anthu enanso ku South Korea omwe anazengedwapo mlandu chifukwa chokana usilikali potsatira zomwe amakhulupirira, akukumananso ndi mavuto omwewo. Mwachitsanzo mu December 2011, a Jin-mo Kang omwe anakwatira mkazi wa ku Japan dzina lake Kotomi, anali pa ulendo wopita ku Japan ndi mkazi wawoyo kukaona achibale. A Kang anawakaniza kulowa m’dziko la Japan chifukwa chakuti makalata awo anasonyeza kuti anamangidwapo chifukwa chokana usilikali. Iwo anakakamizika kusiya mkazi wawo ku Japan n’kubwerera ku South Korea. Ngakhale kuti a Kang anayesetsa kukambirana ndi akuluakulu oona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko, sanawalole kuti apitenso ku Japan.

Dziko la Japan Likufunika Kukhazikitsa Lamulo Lomveka

Dziko la Japan ndi limodzi mwa mayiko amene amaona kuti anthu amene anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, ndi anthu osavomerezeka kulowa m’dzikolo. Komabe patapita nthawi, kazembe wa dziko la Japan ku South Korea anapatsa Gwang-taek Oh chilolezo chopita ku Japan. Gwang-taek Oh anapatsidwa chilolezocho atasonyeza kalata kwa akuluakulu oona za ukazembe. Analemba kalatayo ndi anzake a ku Japan ndipo inali yomuitana kuti akacheze m’dzikolo. Anzakewo anafotokoza kuti adzamusamalira komanso kuti adzakhala ndi udindo pa chilichonse chimene chingachitike pa nthawi imene mnzawoyo adzakhale m’dzikolo. Gwang-taek Oh anapita ku Japan mu July 2016.

Mosiyana ndi dziko la Japan, mayiko ena amalola anthu omwe anaimbidwapo mlandu wokana usilikali, kulowa m’mayikowo. Ndipo mayiko ena amafika mpaka powapezera anthuwo malo abwino okhala. Mwachitsanzo, mayiko ngati Australia, Canada ndi France, amasunga anthu omwe anathawa ku South Korea chifukwa chokana usilikali. Zimenezi n’zogwirizana ndi lamulo latsopano lomwe nthambi yoona za ufulu wa anthu ya bungwe la United Nations linakhazikitsa. Lamuloli limalimbikitsa mayiko kuti “azilola anthu omwe anathawa m’mayiko akwawo chifukwa chokana usilikali, kulowa m’dziko lawo. Mayikowa angachitenso zimenezi kwa anthu omwe anathawa pa zifukwa zomveka monga chifukwa chakuti dziko lawo siliperekanso mwayi wa ntchito zina kwa munthu wokana usilikali kapena chifukwa chakuti m’dzikolo mulibe ntchito zokwanira zomwe zingaperekedwe kwa anthu okana usilikali.” *

Oimira Mboni za Yehova pa nkhani za malamulo, akuyesetsa kukambirana nkhaniyi ndi akuluakulu a boma la Japan. André Carbonneau, ndi loya wapadziko lonse woona za ufulu wa anthu ndipo ananena kuti: “Ngati Gwang-taek Oh analoledwa kulowa m’dziko la Japan ndiye kuti sizingavute kuti azilola anthu enanso okana usilikali kulowa m’dzikolo. Zikungofunika kuti akuluakulu a bomali akhazikitse lamulo limodzi losonyeza kuti anthu okana usilikali, ndi anthu amtendere, si anthu ophwanya malamulo komanso ngakhale kuti anagwirapo ukaidi, aziloledwa kulowa m’dziko la Japan.”

Kodi Boma la South Korea Lisintha Lamulo Lawo?

Mayiko ambiri amaona kuti anthu omwe akugwira ukaidi chifukwa cha chikhulupiriro chawo ndi osalakwa. Kuchokera mu 2006, Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu, yakhala ikudzudzula boma la South Korea chifukwa chomanga anthu omwe amakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Komitiyi inanena kuti boma la South Korea ‘likumanga anthu pa zifukwa zosamveka.’ Komitiyi inagamulanso kuti boma la South Korea lichotse m’kaundula wa anthu ophwanya malamulo, mayina a anthu onse omwe anagwira ukaidi chifukwa chokana usilikali. *

Boma la South Korea likupitirizabe kunyalanyaza zimene komiti ija inagamula. Popeza kuti dzikoli linavomera kukhala nawo mu Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale, limafunika kutsatira malamulo a komitiyi ngakhale malamulowo atakhala kuti sakugwirizana ndi a dziko lawo.

Nzika zambiri ku South Korea zikhalabe zikuvutika, kumangidwa komanso kuonedwa ngati anthu ophwanya malamulo mpaka pamene boma la dzikoli lidzayambe kutsatira mfundo zimene mayiko a padziko lonse anagwirizana pa nkhani yolemekeza ufulu wa anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. * A Mboni za Yehova akuyembekezera nthawi imene dziko South Korea lidzayambe kupereka ufulu kwa anthu okana usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira komanso kusiya kuwaona ngati ophwanya malamulo. Panopa anthu a ku South Korea monga Hyun-jun Gwon ndi Gwang-taek Oh, akukhulupirira kuti akuluakulu a boma ku Japan akhazikitsa lamulo lolola anthu okana usilikali kulowa m’dzikoli.

^ ndime 5 Panopa, dziko la South Korea ndi limodzi pa mayiko 4 okha omwe amaika m’ndende a Mboni za Yehova chifukwa chokana usilikali potengera zimene amakhulupirira. Koma mayiko ambiri, ngakhale kumene ntchito ya usilikali ndi yokakamiza, amalemekeza ufulu wa anthu omwe amakana usilikali ndipo amawapatsa ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali komanso zosayang’aniridwa ndi asilikali.

^ ndime 9 Onani Gawo 24/17 lonena za “anthu okana usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira,” lomwe nthambi Yoona za Ufulu wa Anthu inatulutsa pa October 8, 2013.

^ ndime 12 Onaninso mlandu Na. 1642-1741/2007, wa pakati pa a Jeong et al ndi Dziko la South of Korea, komanso zomwe Komitiyi inagamula pa 24 March, 2011.

^ ndime 14 Zaka 5 zapitazo, dziko la South Korea linamanga anyamata a Mboni okwana 2,701 chifukwa chokana kulowa usilikali potengera zimene amakhulupirira.