Pitani ku nkhani yake

A Gyeong-chan Park ali pamndandanda wa anthu 140 omwe likulu la asilikali linawaika m’gulu la anthu othawa usilikali.

9 JUNE, 2017
SOUTH KOREA

Khoti la ku South Korea Lamva Madandaulo a Anthu Okana Usilikali

Khoti la ku South Korea Lamva Madandaulo a Anthu Okana Usilikali

Pa 1 May 2017, khoti la ku Seoul linanena kuti zimene ofesi ya kulikulu la asilikali ikuchita poipitsa mbiri ya anthu okana usilikali, ponena kuti akuthawa ntchito, zikhoza kubweretsa mavuto aakulu kwa anthuwa. Khotili linagamula kuti a kulikulu la asilikaliwa asiye kuonetsa mayina komanso zinthu zina zokhudza anthu okana usilikali pawebusaiti yawo. A kulikulu la asilikali atsatira zimene khotili linagamula ndipo achotsa mayina ndi mayina ndiponso ma adiresi a anthuwa pawebusaiti yawo.

Sikuti ndi Anthu Othawa Usilikali

Kumayambiriro kwa 2015, akuluakulu a ku ofesi ya asilikali anauza anthu okana usilikaliwa kuti adzafalitsa mayina awo ngati anthu okana usilikali komanso kulemba zinthu zina zokhudza anthuwo. Ofesi ya asilikaliwa inadziwa mayina awo chifukwa m’mbuyomo anthuwa analembera ofesiyi makalata odziwitsa akuluakulu a ofesiyi kuti sangakhale asilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo asankha kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Komabe pa 20 December 2016, ofesiyi inaika pawebusaiti yawo mayina, zaka, ma adiresi komanso zinthu zina zokhudza anthuwa ngati anthu othawa usilikali.

Ofesiyi inalemba pawebusaiti mayina a anthu 237 ngati othawa usilikali ndipo a Gyeong-chan Park omwe ndi a Mboni za Yehova, anadzidzimuka ataona dzina lawo pamndandandawo. Iwo ananena kuti: “Sindinafune kulembetsa usilikali chifukwa cha zomwe ndimakhulupirira komabe ndikudziwa kuti anthu ena sangagwirizane nazo. Komabe pa nthawiyi ndinakhumudwa kwambiri kuona kuti boma linkandiona ngati munthu wothawa usilikali. A kulikulu la asilikali amatidziwa bwino a Mbonife komanso zolinga zathu ndipo amadziwa kuti timakana kulembedwa usilikali osati ngati njira yozembera kuti tisamagwire nawo ntchito za boma.” A Park ananenanso kuti: “Ndisaname, nditangoona dzina komanso adiresi yanga pawebusaitiyi, ndinali ndi nkhawa kuti anthu oipa mtima akhoza kubwera kunyumba kwanga.”

Ponena za kuchotsa mayinawa pawebusaitiyi, a Mboni okwana 140 omwe anaikidwa pamndandandawo, ananena kuti Malamulo a Ntchito ya Usilikali amanena kuti munthu wothawa usilikali, ndi munthu amene satsatira malamulo ndipo amakana usilikali pa zifukwa zosamveka. A Mboniwa anakana zoti ndi anthu othawa usilikali ndipo ananena kuti sikuti amakana usilikali “popanda zifukwa zomveka.” Iwo ananena zimenezi chifukwa malamulo a boma la South Korea amanena kuti ngati munthu wina akukana usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira, umenewo ndi ufulu wake ndipo anthu ena ayenera kulemekeza maganizo ake. Posachedwa Khoti Loona za Malamulo ku South Korea ligamula ngati anthu okana usilikali potsatira zomwe amakhulupirira, akufunika kuwapatsa ufulu kapena ayi.

Boma Likuzunza Anthu Chifukwa Silikutsatira Lamulo Lomwe Limapereka Ufulu

A Mboniwa ananenanso kuti ngakhale akuchitiridwa za nkhanza komanso kuchititsidwa manyazi ndi nzika zina za m’dzikoli, zimenezi sizinawachititse kuti agonje komanso kusintha mmene amaonera usilikali mogwirizana ndi zimene amakhulupirira. M’dziko la South Korea, a Mboni za Yehova oposa 19,000 akhala akuvutika ndi milandu yotereyi ndipo tikaphatikiza zaka zomwe onsewa akhala m’ndende pa zaka 60 zapitazo, zakazo zikuposa 36,000. Anthu amene mayina awo anaikidwa poyera amaona kuti zimene bomali linachita ndi nkhanza. Amaonanso kuti bomali linachita izi kuti aliyense aziwaona ngati anthu ophwanya malamulo ngakhale kuti a Mboniwa akungochita zinthu motsatira chikumbumtima chawo.

Anthu Akuyembekezera Mmene Khoti Lidzaweruzire Mlanduwu

A Mboni za Yehova ku South Korea akusangalala chifukwa choti khoti lamvera madandaulo awo pa nkhani yoti boma likuwaphwanyira ufulu ndipo a Mboniwa akukhulupirira kuti zimene khotili lingagamule zithandizanso kuti likulu la asilikali liyambe kulemekeza ufulu wawo. A Mboniwa akukonzanso zolembera kalata Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku South Korea yopempha kuti bungweli lilembere khotili mmene likuonera nkhaniyi. Khotili likuyembekezeka kudzamvetsera mlanduwu pa 28 June, 2017.