Pitani ku nkhani yake

JULY 13, 2016
SOUTH KOREA

A Mboni za Yehova Omwe Ali M’ndende ku South Korea Aperekanso Madandaulo Ena

A Mboni za Yehova Omwe Ali M’ndende ku South Korea Aperekanso Madandaulo Ena

Kuyambira mu January 2016, amuna oposa 50 a ku South Korea omwe amakana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, apereka madandaulo awo ku gulu lina la bungwe la United Nations lomwe limamva madandaulo a anthu amene amangidwa pa zifukwa zosamveka. Anthu amene apereka madandaulowo anena kuti dziko la South Korea ndi lolakwa chifukwa chowamanga pa zifukwa zosamveka. Iwo ananena kuti kukana usilikali kukugwirizana ndi ufulu wawo wopembedza komanso wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.

Zomwe Zachititsa Kuti Anthuwa Apereke Madandaulo Awo

Magulu awiri a bungwe la United Nations, omwe ndi Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu komanso gulu lomwe limamva madandaulo anthu, ananena kuti anthu amene amamangidwa chifukwa chokana usilikali, “amawamanga pa zifukwa zosamveka.” * Mu 2014, Gulu lina la Bungwe la United Nations, Mfundo zimene linanena gulu lomwe limamva madandaulo a anthu amene akana usilikali. Inanenanso kuti dzikoli lipereke ndalama zachipepeso kwa amene linawamanga komanso kuchotsa maina awo pa mndandanda wa maina a anthu amene ali ndi mbiri yoti analakwira malamulo a dzikolo. Chifukwa cha zimene Komitiyo inanena, a Mboni okwana 682 m’dzikolo apereka madandaulo awo ku gulu la United Nations lomwe limamva madandaulo a anthu amene amangidwa pa zifukwa zosamveka. *

Nkhaniyi Ikuwunikidwa M’dziko Ia South Korea Komanso Mayiko Ena

Gulu la United Nations limeneli likakapereka madandaulowo ku boma la South Korea komanso likamva mbali ya bomalo pankhaniyi, lidzapereka maganizo ake. Ngati gululi lingapezenso kuti boma la South Korea ndi lolakwa, lidzauza bomalo kuti likonze zimene linalakwazo komanso kuti lisiye kumanga anthu amene akana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Kuonjezera pamenepo, khoti lalikulu lomwe limaona nkhani zokhudza malamulo a dziko la South Korea likuwunika kuti lione ngati lamulo loti mwamuna aliyense ayenera kuphunzira usilikali lili logwirizana ndi malamulo a dzikolo, ndipo likuyembekezeka kupereka maganizo ake posachedwapa. Khotili likudziwa kuti madandaulo oposa 600 aperekedwa kale ku gulu la bungwe la United Nations lomwe limamva madandaulo a anthu amene amangidwa pazifukwa zosamveka. Likudziwanso kuti Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu ya Bungwe la United Nations yakhala ikuwuza boma la South Korea mobwerezabwereza kuti liyenera kulemekeza ufulu wa anthu amene safuna kulowa usilikali ndipo liyenera kumapatsa anthu oterewa ntchito zina. Mayiko osiyanasiyana akuyembekezera mwachidwi kuti aone ngati khoti lalikululi ligwirizane ndi mfundo yakuti anthu ali ndi ufulu wokana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

^ ndime 4 Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu,Mfundo zimene linanena gulu lomwe limamva madandaulo a anthu amene amangidwa pa zifukwa zosamveka, Mfundo Na.16/2008 (Turkey), UN Doc. A/HRC/10/21/Add.1, p. 145, ndime. 38 (May 9, 2008). Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu, Zimene inanena pa mlandu wa pakati pa Young-kwan Kim et al. ndi Boma la Republic of Korea, Communication No.2179/2012, UN Doc. CCPR/C/112/D/2179/2012, ndime. 7.5 (October 15, 2014).

^ ndime 4 Mu 2015, anthu amene anakana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira okwana 631 anapereka madandaulo awo, komanso ena okwana 51 aperekanso madandaulo awo mu 2016.