Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

ZOKHUDZA MALAMULO NDIPONSO UFULU WACHIBADWIDWE

Zokhudzana ndi Malamulo ku South Korea

25 JANUARY, 2017

“Chigamulo cha Khoti Chabwino Kwambiri Chaka Chino”

Khoti la Apilo la Gwangju linagamula kuti anyamata atatu ndi osalakwa pa mlandu womwe ankaimbidwa chifukwa chokana usilikali. Aliyense akuyembekezera kuti khoti lapamwamba kwambiri lipereke chigamulo chake.

JULY 13, 2016

A Mboni za Yehova Omwe Ali M’ndende ku South Korea Aperekanso Madandaulo Ena

Dziko la South Korea likupitiriza kuzunza anyamata omwe ndi a Mboni za Yehova powaika m’ndende chifukwa chogwiritsa ntchito ufulu umene ali nawo wopembedza komanso wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.

Kodi Dziko la South Korea Liyamba Kulemekeza Ufulu wa Anthu Wochita Zinthu Mogwirizana ndi Zimene Amakhulupirira?

A Seon-hyeok Kim, omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo sagwira ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, poyamba anawapeza kuti ndi wosalakwa pa mlandu woti ankazemba usilikali. N’chifukwa chiyani khoti la apilo linasintha chigamulochi n’kunena kuti a Kim ndi wolakwa?